Kodi Munayamba Mwasonyezapo Munthu pa Ulendo Woyamba Mmene Timachitira Phunziro la Baibulo?
Anthu ena tikawauza kuti tiziphunzira nawo Baibulo amanena kuti sakufuna kapena amati amaphunziranso Baibulo kutchalitchi kwawo. Iwo samadziwa kuti titaphunzira nawo Baibulo angadziwe zambiri ndiponso angakhale osangalala chifukwa amaganiza kuti njira imene timatsatira pophunzira Baibulo ndi yofanana ndi imene amatsatira kutchalitchi kwawo. Choncho, m’malo mongouza munthu kuti mukufuna kuti muziphunzira naye Baibulo, mungachite bwino kumusonyeza kwa mphindi zingapo pa ulendo woyamba mmene timachitira phunziro la Baibulolo. Tiyerekezere kuti mumadziwa kuphika. M’malo mongowauza anthu kuti mumadziwa kuphika ndipo mungakonde kudzawabweretsera chakudya chimene mumaphika, mungachite bwino kuwalawitsa nthawi yomweyo zimene mumaphikazo. Mungachite zimenezi kwa mphindi zochepa chabe potsatira njira yoyambitsira maphunziro imene ili patsamba 6 mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January, 2006. Mwina mungayambe chonchi:
“Kodi mumaganiza kuti tsiku lina mawu awa adzakwaniritsidwa? [Werengani Yesaya 33:24, ndipo yembekezerani ayankhe.] Talekani ndikusonyezeni mfundo inayake yochititsa chidwi pa nkhani imeneyi.” M’patseni mwininyumbayo buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, ndipo musonyezeni ndime 22 imene ili patsamba 36. Werengani funso limene lili mmunsi mwa tsambali, ndipo muuzeni mwininyumbayo kuti apeze yankho lake mukamawerenga ndimeyo. Kenako funsaninso funsolo, ndipo mvetserani mwininyumbayo akamayankha. Werengani ndi mwininyumbayo lemba linanso la m’ndimeyo. Funsani funso loti mudzayankhe pa ulendo wotsatira, ndipo gwirizanani tsiku ndi nthawi yeniyeni yoti mudzakumanenso. Apa ndiye kuti basi mwayambitsa phunziro la Baibulo.