Mmene Tingayambitsire Maphunziro a Baibulo ndi Anthu Omwe Timawagawira Magazini
1. Kodi cholinga chathu pogawira magazini n’chotani?
1 Nthawi zambiri Loweruka timagawira magazini ya Nsanja ya Olonda ndi ya Galamukani! Koma kuchita zimenezi ndi chiyambi chabe cha mmene tingakwaniritsire cholinga chathu chophunzitsa choonadi anthu a mtima wabwino. Nazi njira zina za mmene tingagawirire buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani paulendo wobwereza ndi kuyamba phunziro la Baibulo. Njira zimenezi mungazisinthe kuti zigwirizane ndi zochitika za m’gawo lanu ndiponso mungazinene m’mawu anuanu. Mungagwiritsenso ntchito njira ina imene mukuona kuti ndi yothandiza.
2. Kodi tingagwiritse ntchito motani zomwe zili pa masamba oyambirira a m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kuyambitsa phunziro la Baibulo?
2 Gwiritsani Ntchito Zomwe Zili pa Masamba Oyambirira: Mukapanga ulendo wobwereza, munganene kuti: “Magazini amene ndinakusiyirani amafotokoza za m’Baibulo. Taonani chifukwa chake kuwerenga Baibulo n’kofunika kwambiri.” Werengani Yesaya 48:17, 18; Yohane 17:3 kapena lemba lina loyenerera. Mukasonyeza mwininyumba buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndi kum’patsa limodzi, munganene zotsatirazi:
◼ “Baibulo limatipatsa chiyembekezo chenicheni cha zinthu zabwino m’tsogolo.” Sonyezani mwininyumba masamba 4 ndi 5 ndipo mufunseni kuti: “Kodi ndi lonjezo liti mwa malonjezo awa lomwe mungakonde litakwaniritsidwa?” Musonyezeni mutu umene umafotokoza lonjezo la m’Malemba limene wasankha, ndipo mwachidule kambiranani ndime imodzi kapena ziwiri ngati akulola.
◼ Kapena munganene kuti, “Baibulo limayankha mafunso ofunika kwambiri amene timakhala nawo pamoyo.” Musonyezeni tsamba 6 ndi kum’funsa ngati anayamba wadzifunsapo funso lililonse pa mafunso omwe ali munsi mwa tsambali. Tsegulani mutu umene ukuyankha funsolo, ndipo mwachidule kambiranani ndime imodzi kapena ziwiri.
◼ Kapena mungatchule mitu ina yomwe ili patsamba la za m’katimu ndipo mufunseni nkhani imene ikum’sangalatsa. Tsegulani mutu umenewo ndipo mwachidule musoyenzeni mmene timachitira phunziro la Baibulo.
3. Kodi tingayambe motani phunziro la Baibulo tikagawira magazini omwe akufotokoza za (a) kuipiraipira kwa zinthu m’dzikoli? (b) banja? (c) kudalirika kwa Baibulo?
3 Musiyireni Funso Paulendo Wanu Woyamba: Njira ina ndi yoti paulendo wanu woyamba mum’konzekeretse mwininyumba kuti mudzabweranso. Mwininyumba akalandira magazini, m’funseni funso ndipo muuzeni kuti mudzaliyankha paulendo wotsatira. Onetsetsani kuti mwapanga makonzedwe otsimikizirika oti mudzabweranso, ndipo yesetsani kuchita zimenezo. (Mat. 5:37) Mukapitakonso, kumbutsani mwininyumba funso limene munam’siyira ndipo mwachidule werengani ndi kukambirana yankho la funsolo m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. M’patseni buku kuti iyenso azikutsatirani. Nazi zitsanzo zina:
◼ Ngati magazini imene mwagawira ikufotokoza za kuipiraipira kwa zinthu m’dzikoli, munganene kuti, “Ndikadzabweranso tingadzakambirane yankho la m’Baibulo la funso ili, Kodi Mulungu adzasintha zinthu motani padziko lapansi?” Mukabwererako, sonyezani mwininyumba tsamba 4 ndi 5. Kapena mungafunse funso loti, “Kodi masoka n’cholinga cha Mulungu?” Ndiyeno mukabwererako, sonyezani mwininyumba ndime 7 ndi 8 m’mutu 1.
◼ Ngati magazini imene mwagawira ikufotokoza za banja, musanachoke mungafunse funso loti, Kodi aliyense pabanja angachite chiyani kuti banjalo lizisangalala?” Mukabwererako kambambiranani ndime 4 m’mutu 14.
◼ Ngati magazini imene mwagawira ikufotokoza za kudalirika kwa Baibulo, mungafunse funso lotsatirali loti mudzakambirane paulendo wotsatira, “Kodi Baibulo n’lolondola pankhani za sayansi?” Mukabwererako, kambiranani ndime 8 m’mutu 2.
4. Kodi tingatani ngati mwininyumba sanalandire buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani?
4 Nthawi iliyonse imene mumaliza kukambirana ndi munthuyo, funsani funso lina loti mudzayankhe paulendo wotsatira. Mukayamba kuphunzira bukuli mokhazikika, liphunzireni bwinobwino motsatira ndondomeko ya mitu yake kuyambira ndi woyamba. Nanga bwanji ngati mwininyumba sanafune kulandira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani? Mungapitirizebe kukam’patsa magazini ndi kumakambirana naye zinthu za m’Malemba. Pamene mukum’thandiza kukhala ndi chidwi, m’kupita kwa nthawi angavomere kuti muziphunzira naye Baibulo.
5. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti anthu tisamangowasiyira chabe magazini?
5 Magazini ya Nsanja ya Olonda ndi ya Galamukani! angalimbikitse munthu kuphunzira zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni. Motero, yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndi anthu omwe amalandira magazini athu. Mwakuchita zimenezi, tidzatsatira malangizo a Yesu oti ‘tipange ophunzira ndi kuwaphunzitsa.’—Mat. 28:19, 20.