Tingathe Kuyambitsa Phunziro kwa Anthu Amene Timawapatsa Magazini
1. N’chifukwa chiyani gulu la Yehova limatilimbikitsa kuti tikhale ndi anthu omawapatsa magazini nthawi zonse?
1 Anthu ena safuna kuti tiziphunzira nawo Baibulo, komabe amasangalala kwambiri kuwerenga magazini athu. Choncho kuyambira kale, gulu la Yehova lakhala likulimbikitsa ofalitsa kuti azipereka magazini kwa anthu oterewa. Anthu amenewa akawerenga magazini athu kwa nthawi yaitali, nthawi zambiri zimapangitsa kuti ayambe kukonda Mawu a Mulungu. (1 Pet. 2:2) Pakapita nthawi, amapeza mfundo inayake imene imawachititsa chidwi mpaka kuvomereza kuti tiziphunzira nawo Baibulo.
2. Kodi tingakulitse bwanji chidwi cha anthu amene timawapatsa magazini?
2 ‘Muzithirira’ Mbewu za Choonadi: Mukapita kwa anthu amenewa, musangowapatsa magazini n’kuchoka. Yesetsani kucheza nawo mwachidule kuti mudziwane nawo. Zimenezi zingakuthandizeni kudziwa zokhudza moyo wawo, zimene amakonda komanso zomwe amakhulupirira. Izi zidzakuthandizani kudziwa zoyenera kukambirana nawo. (Miy. 16:23) Musanapite kukawapatsa magazini, muzikonzekera kaye. Ngati n’zotheka, fotokozani mwachidule mfundo ina imene ili m’magaziniyo komanso lemba logwirizana ndi mfundoyo. Mukamachita zimenezi ndiye kuti mukuthirira mbewu za choonadi zimene zili mu mtima mwawo. (1 Akor. 3:6) Lembani deti limene mwapitako, chilichonse chomwe mwawasiira, nkhani imene mwakambirana komanso lemba lomwe mwawerenga.
3. Kodi kwa anthu amene timawapatsa magazini, tizipitako pakapita nthawi yaitali bwanji?
3 Kodi Tizipitako Pakapita Nthawi Yaitali Bwanji? Muyenera kumapitako mwezi uliwonse kuti mukawapatse magazini atsopano. Komabe, mogwirizana ndi mmene zinthu zilili kwa inuyo komanso chidwi cha anthuwo, mungathe kumapitako pafupipafupi. Mwachitsanzo pakatha mlungu umodzi kapena iwiri, mungapiteko n’kuwauza kuti, “Ndabwera kuti tikambirane mwachidule mfundo ina m’magazini amene ndinakusiyirani aja.” Zimenezi zingachititse kuti achite chidwi ndi nkhaniyo n’kufuna kuiwerenga. Ngati awerenga kale, mungawafunse maganizo awo pa nkhaniyo n’kukambirana nawo mwachidule. Komanso ngati amasangalala kwambiri ndi magazini athu, moti amamaliza kuwawerenga mwezi usanathe, mungapitekonso n’kuwapatsa kapepala, kabuku kapena buku limene tikugawira mwezi umenewo.
4. Kodi tizichita chiyani nthawi zonse kuti tidziwe ngati anthu amene timawapatsa magazini akufuna kuyamba kuphunzira Baibulo?
4 Musadikire kuti adzakuuzeni okha kuti akufuna kuyamba kuphunzira Baibulo. Yambani ndi inuyo. Ngakhale zitakhala kuti poyamba ananena kuti sakufuna kuphunzira Baibulo, nthawi zonse asonyezeni nkhani zakuti, “Kuyankha Mafunso a M’Baibulo” zimene zimakhala mu Nsanja ya Olonda kuti muone ngati angakonde kuti mukambirane nkhanizi. Mwina mukhoza kuyamba nawo phunziro lachidule. Komabe ngati simungathe kuyamba kuphunzira nawo, mungapitirizebe kuwapititsira magazini n’cholinga choti m’kupita kwa nthawi adzakhale ndi chidwi chofuna kuphunzira.