Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Pezani Anthu Oti Muziwapatsa Magazini Mwezi Uliwonse
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’Kofunika?: Anthu ena amakonda kuwerenga magazini athu koma safuna kuti tiziphunzira nawo Baibulo. Mwina safuna kuphunzira chifukwa amaona kuti ali kale ndi chipembedzo chawo kapena amaona kuti alibe nthawi yophunzira Baibulo. Komabe, akamawerenga magazini athu nthawi zonse, akhoza kufuna kudziwa zambiri. (1 Pet. 2:2) Nkhani ina ya m’magazini athu, ikhoza kuwachititsa chidwi kapena zinthu pa moyo wawo zikhoza kusintha. Choncho tikamawayendera nthawi zonse, angayambe kumasuka nafe ndipo zimenezi zingatithandize kudziwa zimene amakonda komanso zomwe zimawadetsa nkhawa. Kenako, tikhoza kuyamba kuphunzira nawo Baibulo.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Lembani mayina a anthu omwe mukuganiza kuti mungamawapatse magazini mwezi uliwonse. Apititsireni magazini atsopano ndipo auzeni kuti mudzawapatsanso magazini a mwezi wamawa.