Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/98 tsamba 8
  • “Kufesa Mbewu za Ufumu” Panjira za Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kufesa Mbewu za Ufumu” Panjira za Magazini
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Tingathe Kuyambitsa Phunziro kwa Anthu Amene Timawapatsa Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Gwiritsirani Ntchito Magazini Athu m’Njira Yabwino Koposa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Pezani Anthu Oti Muziwapatsa Magazini Mwezi Uliwonse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Gawirani Magazini mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 10/98 tsamba 8

“Kufesa Mbewu za Ufumu” Panjira za Magazini

1 Nyimbo 133 m’buku la Imbirani Yehova Zitamando ili ndi mutu wakuti “Kufesa Mbewu za Ufumu.” Inazikidwa pafanizo la Yesu limene limayerekezera ntchito yopanga ophunzira ndi kufesa mbewu. (Mat. 13:4-8, 19-23) Mawu a nyimboyi amati: “Kuti zigwere panthaka yabwino/Zimadalira pa inu.” Kodi tingachitenji kuti utumiki wathu ukhale wogwira mtima kwambiri? Njira imodzi ndi kuyambitsa ndi kusungabe njira ya magazini.

2 Njira ya magazini ingakwaniritse zinthu zambiri. (1) Kupanga maulendo pamilungu iŵiri iliyonse kumakuthandizani kuti mupange ubwenzi ndi munthu wokondwererayo. (2) Nthaŵi zonse munthuyo mumampatsa chidziŵitso chopulumutsa moyo chopezeka mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! (3) Mwa zimene mumakambitsirana ndi munthuyo mungamthandize kukhala ndi chilakolako cha choonadi cha Malemba, zimene zingatsogolere kuphunziro la Baibulo.—1 Pet. 2:2, NW.

3 Mmene Mungayambire Njira ya Magazini: Nthaŵi zonse munthu akachita chidwi ndi magazini, mfotokozereni kuti nkhani zabwino zimatuluka m’kope lililonse ndipo mudzakhala okondwa kumampatsira makopewo milungu iŵiri iliyonse. Mutachoka, lembani dzina ndi adresi ya munthuyo, deti limene munamfikira, deti la makope amene mwamgaŵira, nkhani imene munamsonyeza, ndi nkhani zimene zinamsangalatsadi munthuyo.

4 Mungayambe njira ya magazini ndi anthu ochepa chabe. Ndiyeno yesani kuikulitsa mwa kuwonjezerapo anthu ena amene mumawagaŵira magazini. Pamene njira yanu ikula, mungakonze kuti muzifikira anthu molingana ndi dera limene akukhala kotero kuti musamavutike kuwazungulira. Sungani zolembedwa zabwino za makope amene mwagaŵira kwa aliyense ndiponso pamene munawagaŵira. Lembaninso nsonga zimene mumakambirana ndi za mmene mungakulitsire chidwi cha munthuyo paulendo wanu wotsatira.

5 Phatikizanipo Anthu Amalonda ndi Apantchito: Zokumana nazo zaonetsa kuti ogulitsa m’sitolo ndi anthu ena apantchito angamalandire magazini athu mokhazikika. Mkulu wina panjira yake ya magazini panali meya wa tauni imene amakhala. Wofalitsa wina anayamba phunziro ndi mwini wake wa kampani ina yogulitsa zinthu zomangira nyumba yemwe anali ndi zaka 80 zakubadwa pambuyo pomakampatsa magazini kwa zaka khumi zathunthu!

6 Mlongo wina mpainiya analoŵa m’sitolo ndi kupezamo mwamuna ndi mkazi wake amene sanamlandire bwino. Komabe, popeza kuti anatenga magazini, iye anaganiza zophatikiza banjali panjira yake ya magazini. Patapita nthaŵi, mlongoyo anafuna kuwaleka chifukwa sanali aubwenzi ndipo sanali kunena zambiri, ngakhale atawafunsa malingaliro awo. Koma mlongoyo anapemphera za nkhaniyo ndipo potsirizira pake anagaŵira banjalo buku la Kukhala ndi Moyo. Ataliŵerenga, mkaziyo anati: “Ndachipeza choonadi tsopano!” Anayamba phunziro la Baibulo, ndipo kenako banjalo linabatizidwa. Kulimbikira kwa mpainiyayo kunabaladi chipatso chabwino.

7 Kupanga Maulendo Obwereza: Mutalandira magazini atsopano, ŵerengani nkhani zonse. Funani nsonga zimene zikasangalatsa munthu aliyense amene ali panjira yanu ya magazini. Ndiyeno mutabwererako munganene kuti: “Pamene ndinali kuŵerenga nkhani iyi, ndinali kuganiza za inuyo ndi mmene ingakusangalatsireni.” Ofalitsa a misinkhu yonse angakhale ndi njira za magazini. Ngakhale mwana akhoza kunena kuti: “Ndili wokondwa kukuonaninso. Makope anu atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! afika. Ndikukhulupirira kuti mudzaikonda nkhani iyi yakuti . . .”

8 Apangitseni kulakalaka kudzaŵerenga nkhani za m’magazini otsatira mwa kuwasonyeza bokosi lakuti “M’Kope Lathu Lotsatira.” Patatuluka nkhani zimene mbali zake zina zidzatuluka m’makope otsatira, asonyezeni zimenezi ndipo alimbikitseni kuti asaphonye mbali iliyonse. Musaiŵale kuti nthaŵi zonse pamene mukapereka magazini kwa munthu amene ali panjira yanu ya magazini, mungaŵerenge ulendo wobwereza. Koposa zonse, kumbukirani kuti cholinga chathu ndi kusandutsa maulendo ameneŵa kukhala maphunziro a Baibulo.

9 Yenderani Anthu Amene Ali Panjira Yanu Mokhazikika: Mungazungulire njira yanu ya magazini panthaŵi iliyonse imene ili yoyenerera—mmaŵa wa tsiku la mkati mwa mlungu, cha kumasana, ndi kachisisira madzulo, kapena pamapeto a mlungu mutachoka kuntchito ya kunyumba ndi nyumba. Ngati simutha kuzungulira njira yanu chifukwa cha kudwala kapena kuti mwapita kuholide, uzani wofalitsa wina m’banja lanu kapena m’mpingo wanu kuti akakuperekereni magaziniwo. Mwa njirayi, anthu amene mumakawapatsa magazini adzalandira magaziniwo panthaŵi yake.

10 Njira imodzi yofesera mbewu za Ufumu ndiyo kukapereka Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa anthu amene ali panjira yanu ya magazini. Pamene mukuwaphunzitsa choonadi cha Malemba, angazindikire mawu a Ufumu ndipo angafike pobala zipatso za Ufumu pamodzi nanu.—Mat. 13:8, 23.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena