Oyang’anira Amene Amatitsogolera—Mlembi
1 Mlembi wa mpingo ndi wofunikira kwambiri poonetsetsa kuti ‘zonse zikuchitika koyenera ndi kolongosoka.’ (1 Akor. 14:40) Monga mmodzi wa Komiti Yautumiki Yampingo, amasamalira makalata a mpingo ndi zolembedwa zofunikira. Ngakhale kuti ntchito zake sizingaonekere kwa aliyense monga ngati za akulu ena, ntchito yake njofunika kwambiri ndipo njoyamikirika.
2 Pamene mpingo ulandira makalata kuchokera ku Sosaite kapena kwa anthu ena, mlembi ndiye amawasamalira ndi kuona kuti ayankhidwa ngati kuli kofunika kutero. Amaonetsetsa kuti makalata amene akulandiridwa akuperekedwa kwa akulu ena kuti awaŵerenge ndiyeno iye amawaika m’faelo kaamba ka za mtsogolo. Amapenda mafomu oodera magazini ndi mabuku ndi kuwatumiza ku Sosaite. Amayang’anira amene amasamalira maakaunti ndi masabusikripishoni ndiponso nkhani zonse zokhudzana ndi msonkhano wachigawo.
3 Popeza kuti mlembi amayenera kutumiza lipoti la utumiki wakumunda la mpingo ku Sosaite pofika patsiku la chisanu ndi chimodzi la mwezi uliwonse, nkoyenereradi kuti tonsefe tizipereka lipoti lathu la ntchito ya m’munda mwamsanga pamapeto a mwezi uliwonse. Ndiyeno amalemba malipoti autumiki pa makadi a Cholembapo Ntchito za Wofalitsa cha Mpingo. Wofalitsa aliyense angapemphe kuti aone mmene wakhala akugwirira ntchito yake.
4 Pamene wofalitsa abwera kapena asamuka mu mpingo, mlembi amafunsa kapena kutumiza kwa akulu a mpingo winawo kalata yodziŵikitsa wofalitsayo pamodzi ndi makadi ake a Cholembapo Ntchito za Wofalitsa cha Mpingo.—Uminisitala Wathu, mas. 104-5.
5 Mlembi amapenda ntchito za apainiya, amadziŵitsa akulu ena, makamaka woyang’anira utumiki, za mavuto alionse amene apainiyawo akukumana nawo. Amadziŵitsa ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo za ofalitsa amene ali osakhazikika mu utumiki wakumunda. Onse mlembi ndi woyang’anira utumiki amatsogolera poyesayesa kusamalira amene ali ofooka.—Utumiki Wathu Waufumu, November 1987, tsa. 1 (Chingelezi).
6 Pokhala titazindikira bwino ntchito za mlembi, tichitetu zimene tingathe kumthandiza kuti udindo wake aziukwaniritsa mosavuta.—1 Akor. 4:2.