Chikumbutso kwa Mlembi ndi Woyang’anira Utumiki
Chaka chilichonse chilengezo cha mu Utumiki Wathu Waufumu wa February chimauza mlembi ndi woyang’anira utumiki “kupenda ntchito za apainiya okhazikika onse.” Kodi chifuno chake cha kupenda kumeneku nchiyani? Ndicho kudziŵa amene angafunikire chithandizo cha kukwaniritsa chofunika cha maola chaka chisanathe.
Apainiya okhazikika afunikira kuthera maola 1,000 chaka chilichonse mu utumiki. Pofika kumapeto kwa February, apainiya ena amapeza kuti atsala kumbuyo, ndipo zimenezi zingawafooketse. Akulu kaŵirikaŵiri angakhale othandiza kwa apainiya, akumawapatsa chilimbikitso ndi malingaliro ogwira ntchito. Zimenezi zingathandize kwambiri apainiya kukhala okhoza kukwaniritsa chofunika chawo cha pachaka, apo phuluzi akhoza kuchoka pampambo.
Apainiya amayamikiradi chisamaliro chenicheni cha akulu pankhani imeneyi. Mpingo udzapindulanso mwa kukhala ndi apainiya amene ali achimwemwe mu utumiki wawo, akumamamatira mokhulupirika pa ntchito yawo.