Limbikirani Muutumiki Waupainiya
MBONI ZA YEHOVA pafupifupi 4,500,000 zikulengeza mbiri yabwino padziko lonse. Pakati pawo pali apainiya, kapena olengeza Ufumu anthaŵi yonse oposa 600,000. Awo amene ali m’gulu la apainiya limeneli amaphatikizapo amsinkhu wa pansi pa zaka 13 kufika kwa opumulitsidwa pantchito a m’zaka zawo za m’ma 90. Iwo ali ndi ziyambi ndi mikhalidwe ya moyo yosiyanasiyana.
Mosakayikira, alaliki anthaŵi yonse onsewa amafuna kupambana muutumiki waupainiya. Ambiri amafuna kuupanga kukhala ntchito yawo ya moyo wonse. Ena ali osakhoza kuchita zimenezo pazifukwa zina. Komabe, ena akhoza kupitiriza upainiya mosasamala kanthu za mavuto a ndalama, matenda, zolefula, ndi mavuto ena. Motero kodi ndimotani mmene alaliki anthaŵi yonse angapiririre mavuto oterowo ndi kulimbikirabe muutumiki waupainiya?
Kukwaniritsa Zosoŵa Zandalama
Apainiya ambiri amagwira ntchito yakuthupi kuti alipirire zofunika, monga momwe anachitira Paulo. (1 Atesalonika 2:9) M’mbali zambiri za dziko, amayang’anizana ndi kukwera kofulumira kwa mitengo ya chakudya, zovala, nyumba, ndi zoyendera. Kaŵirikaŵiri kumakhala kovuta kupeza ntchito ya maola ochepa imene amafuna. Ngati zipezeka, ntchito zoterozo kaŵirikaŵiri zimawapatsa malipiro ochepa, popanda inshuwalansi ya chipatala.
Ngati tipitiriza ‘kuthanga tafunafuna Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake,’ tikhoza kukhala ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzatigaŵira zosoŵa zathu zakuthupi. Chotero, pamene akhala m’vuto la ndalama, apainiya afunikira ‘kusadera nkhaŵa za tsiku lotsatira.’ (Mateyu 6:25-34) Ngakhale kuti amapanga kuyesayesa kowona mtima kuthetsa mavuto oterowo, chikhulupiriro cholimba mwa Yehova chidzawachotsera nkhaŵa zosayenera.
Pamene munthu ayang’anizana ndi mavuto a ndalama, mwinamwake zowonongedwa zikhoza kuchepetsedwa. Atasintha bajeti, kungakhale kotheka kukwaniritsa zosoŵa, koma osati zofuna wamba zakuthupi. Kuti achepetsepo ndalama zowonongedwa, apainiya ena amakhala m’nyumba imodzi ndi Akristu ena. Kuti athandize ana awo kuchita upainiya, nthaŵi zina makolo amapereka malo okhala kwaulere kapena pamalipiro otsika. Ena amathandiza apainiya ndi chakudya ndi ndalama zoyendera. Koma apainiya samafuna kukhala chothodwetsa kwa ena, chifukwa chakuti ali ndi thayo la Malemba la kudzichilikiza okha.—2 Atesalonika 3:10-12.
Ndalama zoyendera zingachepetsedwe mwakugaŵana zowonongedwa ndi apainiya ena. Ngati apainiya aŵiri ali ndi galimoto, iwo angapitire pamodzi m’ntchito yolalikira kumalo amodzi, akumagwiritsira ntchito galimoto limodzi ndi kuchepetsa mtengo wa kuyendetsa galimoto ziŵiri. Apainiya amene alibe galimoto angapange gulu limodzi ndi awo okhala ndi galimoto zawo ndi kugaŵana kulipirira ndalama zoyendera. Ndalama zoyendera zikhoza kuchepetsedwanso mwakufola magawo apafupi mwakuyenda pansi. M’maiko ambiri apainiya amagwiritsira ntchito zoyendera za onse zotsika mtengo.
Newton Cantwell ndi mkazi wake anali pakati pa awo amene analaka mavuto andalama ndi kulimbikirabe muutumiki wa nthaŵi yonse. Iwo anagulitsa famu yawo ndi kuyamba upainiya mu 1932 pamodzi ndi ana asanu ndi mmodzi mwa ana awo asanu ndi aŵiri, mkati mwa Kutsika Kwakukulu kwa Chuma Chadziko. “Sipanapite nthaŵi yaitali pamene ndalama zathu zinatha zimene tinagulitsira famu yathu—makamaka chifukwa cha kulipira madokotala,” analemba motero Mbale Cantwell. “Tikukumbukira kuti pamene tinapita ku gawo lathu lachiŵiri, tinali ndi ndalama zokwanira kulipirira nyumba ya lendi kwa milungu iŵiri yokha, ndi madola asanu otsalapo. Komabe, tinadziŵa kuti Yehova akagaŵira malinga ngati tinachita utumiki wathu mowona mtima. . . . Tinaphunzira kusawawanya ndalama m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, pamene tinasamukira ku gawo latsopano, ndinali kulankhula kwa eni malo ogulitsa petulo kuti tinali kuyendetsa galimoto zitatu tsiku lililonse m’ntchito yathu Yachikristu. Zimenezi zinatitheketsa kumagula petulo pamtengo wotsika. Ana athu mwamsanga anaphunzira kukonza galimoto zathu, akumasungitsa ndalama zambiri zomwe tikanalipira ku garaji.” Chotero banja la a Cantwell linapirira mavuto a ndalama mwachipambano ndi kulimbikirabe muutumiki wanthaŵi yonse. Mbale Cantwell anali adakali pa ndandanda ya apainiya pamene anamwalira pausinkhu wa zaka 103.
Kupeza Ntchito ya Maola Ochepa
Apainiya ambiri amadzichilikiza m’zandalama mwakugwira ntchito za maola ochepa. Kuti adzichilikize muutumiki ku Korinto, Paulo anagwira ntchito monga wosoka mahema limodzi ndi okhulupirira anzake Akula ndi Priskila. (Machitidwe 18:1-11) Lerolino, abale auzimu kaŵirikaŵiri amakhala achimwemwe kupatsa apainiya ntchito ya maola ochepa. Apainiya ena amapeza ntchito zoterozo ku makampani amene amapatsa ntchito zaganyu. Chikhulupiriro mwa Mulungu nchofunika, ndiponso pemphero lowona mtima kaamba ka chitsogozo chake m’kupanga zosankha zofuna ntchito.—Miyambo 15:29.
Mpainiya wina anati, “Nditapeza chilimbikitso chachikulu mwa kupenda kochitidwa ndi mapemphero, ndinauza mkulu wantchito kuti ntchito yanga yautumiki ili thayo langa lofunika kwambiri ndi kuti sindinali wokhoza kugwira ntchito ya tsiku lonse. Pa Lachitatu mlungu wotsatira, ndinafunsidwa kuti ndilingalirenso za ntchitoyo koma ya maola ochepa. Ndinavomera mwachimwemwe.” Musachepetse mphamvu ya pemphero, ndipo chitani zinthu mogwirizana ndi mapemphero anu.
Apainiya angakupeze kukhala kwanzeru kuuza ofuna kuwalemba ntchito kuti chimene akufunira ntchito ya maola ochepa ndicho kudzichilikiza muutumiki. Angatchule masiku amene angagwire ntchitoyo ndi unyinji wa maola pamlungu amene angawathere pantchitoyo. Alongo aŵiri paubale wawo anagaŵana ntchito ya tsiku lonse pakampani ina ya zamalamulo, akumalola aliyense wa iwo kugwira ntchito kwa masiku aŵiri ndi theka pamlungu. Zimenezi zinawachilikiza monga apainiya kufikira pamene anapita ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ndi kulandira magawo aumishonale.
Ntchito zosiyanasiyana zololedwa Mwamalemba zikhoza kupezedwa mwakulankhula kwa okhulupirira anzanu ndi ena kapena mwakuyang’ana pa zilengezo za m’nyuzipepala. Kudzichepetsa nkofunika, pakuti kungaletse apainiya kukhala osankha mopambanitsa ntchito imene angakonde kuchita. (Yerekezerani ndi Yakobo 4:10.) Kuti apitirize kuchita upainiya angafunikire kugwira ntchito yakuthupi imene anthu ena amaiona kukhala yotsika kapena yaulebala. Ngati ntchito yoteroyo ilandiridwa koma mukufuna inayake, m’kupita kwanthaŵi kukhoza kukhala kotheka kusintha ntchito.
Kudwala ndi Zolefula Zina
Ena amaleka upainiya chifukwa cha kudwala matenda aakulu. Komabe, ngati apainiya safulumira kuleka, angapeze kuti nthendayo ikhoza kuchiritsidwa kapena thanzi lawo likhoza kuwongokera ndi kuwalola kupitiriza upainiya. Ambiri akhoza kuchitabe upainiya mosasamala kanthu za matenda chifukwa chakuti amalandira chithandizo cha mankhwala, kutsatira kadyedwe kowayenera, ndi kupuma mokwanira ndi machitachita olimbitsa thupi. Woyang’anira woyendayenda wina anaona mlongo yemwe ndi mpainiya amene anali ndi nthenda yakutupa mfundo zathupi kwakuti anali kuthandizidwa kuyenda muutumiki wa kunyumba ndi nyumba. (Machitidwe 20:20) Komabe, iye ndi mwamuna wake anachititsa maphunziro a Baibulo apanyumba 33 ndipo anathandiza anthu 83 kulandira chowonadi cha Mulungu. Thanzi lake linakhala bwino m’kupita kwa nthaŵi, ndipo anapezekapo pa Sukulu Yautumiki Waupainiya zaka 11 pambuyo pake.
Kulefulidwa kungapangitse ena kuleka utumiki waupainiya. (Miyambo 24:10) Mpainiya wina anauza woyang’anira woyendayenda kuti: “Ndidzaleka upainiya. . . . Ndili ndi ngongole zambiri zofunikira kulipira.” Iye anafunikira magalasi amaso a mtengo wa madola 20. “Kodi mudzaleka upainiya chifukwa cha kusoŵa 20 dola?” anafunsa motero woyang’anirayo. Anapereka lingaliro lakuti mpainiyayo agwire ntchito pafamu ya khofi ya kumaloko, apeze 20 dola, ndiyeno akagule magalasiwo ndi kupitiriza upainiya. Pamene anapitiriza kukambitsirana anapeza kuti vuto lalikulu linali kulefulidwa chifukwa cha kukonzetsa galimoto lake kodya ndalama zambiri. Lingaliro linaperekedwa lakuti mpainiyayo achepetse zowonongedwa mwakuyenda ndi galimoto lake maulendo aafupi m’malo mwakufika kutali kwambiri. Analimbikitsidwanso kusunga mkhalidwe wake wauzimu. Mpainiyayo anagwiritsira ntchito uphunguwo ndipo pambuyo pa miyezi isanu ndi umodzi anaitanidwa kukapezekapo pa Sukulu ya Gileadi. Atamaliza maphunzirowo anagaŵiridwa kudziko lakutali kumene anakatumikira mokhulupirika kwa zaka zambiri kufikira imfa yake. Inde, madalitso aakulu kaŵirikaŵiri amakhalapo ngati sitilola kulefulidwa kutigonjetsa koma kukumbukira kuti Yehova ali nafe.
Onani Mwaŵi Wanu Wautumiki Monga Chuma
Mosasamala kanthu za ziyeso, monga ngati zosoŵa ndi nthaŵi zakusoŵa chakudya, Paulo anaona utumiki wake kukhala chuma. (2 Akorinto 4:7; 6:3-6) Poyang’anizana ndi mavuto ndi chizunzo lerolino, atumiki a Yehova ambiri mu Afirika, Asia, Kummaŵa kwa Ulaya, ndi kwina kulikonse apitirizabe ndi mwaŵi wawo waupainiya. Chotero, pamene mukumana ndi ziyeso, yesayesani kulimbikira m’mwaŵi wanu wautumiki umenewu, kuchitamando cha Yehova.
Apainiya ambiri anali okhoza kuloŵa ntchito yolalikira yanthaŵi yonse chifukwa chakuti anapeputsa njira ya moyo wawo. Mofanana ndi Paulo, iwo anakaniza zonyengerera za zinthu zakuthupi ndi kukulitsa chikhutiro cha ‘zakudya ndi zofunda.’ Kuti alimbikire muutumiki waupainiya, afunikira kukhalabe okhutira ndi zinthu zofunika. (1 Timoteo 6:8) Chimwemwe chimabwera ndi kuona mwaŵi wathu wopatsidwa ndi Mulungu kukhala chuma, kuuika pamwamba pa zinthu zakuthupi.
Nachi chitsanzo: Anton Koerber anapatsidwa mwaŵi wakuimira zinthu Zaufumu kwa akuluakulu a boma mu Washington, D.C. Iye anatumikira monga mpainiya kwa nthaŵi yakutiyakuti ndipo anali woyang’anira dera m’ma 1950. Anzake ena akale ochita nawo malonda anamfikira namuuza kuti anali okhoza kumpangitsa kupeza madola okwanira miliyoni imodzi. Koma kuti zimenezo zitheke, zinafuna kuti iye apereke nthaŵi yake yonse m’malonda kwa pafupifupi chaka chimodzi. Atapempherera chitsogozo ndi mzimu wa maganizo olama, iye anati: “Sikutheka kuti ndileke mwaŵi wanga wabwino koposa wa kutumikira Yehova kwa chaka chimodzi, ayi, osati ngakhale kaamba ka ndalama zonse zili m’dziko. Kutumikira abale anga kunoko ku Washington nkwamtengo wapatali kwa ine, ndipo ndidziŵa kuti kunoko ndili ndi dalitso la Yehova. Mosakayikira ndikhoza kupeza madola miliyoni imodzi, koma kodi pakutha kwa chaka cha moyo woterowo, ndidzakhala munthu wotani mwauzimu, kapena ngakhale mwakuthupi?” Motero iye anakana mwaŵi umenewo. Kuona mwaŵi wawo kukhala wamtengo wapatali mwanjira yofananayo kumathandiza ambiri kulimbikira muutumiki waupainiya.
Ndimadalitso aakulu otani nanga amene apainiya amakhala nawo! Lili dalitso kuthera maola ambiri mukulankhula ponena za ufumu waulemerero wa Yehova. (Salmo 145:11-13) Chifukwa cha kuthera nthaŵi yaikulu kwambiri muutumiki, apainiya ali ndi dalitso la kudzetsa chitonthozo chauzimu pa osauka ndi otsenderezedwa, odwala kapena oferedwa, ndi ena opsinjika kwambiri ndi ofunikira chiyembekezo. Chifukwa chake, ngati mikhalidwe itilola kuloŵa ntchito yolalikira yanthaŵi yonse, tidzasangalala ndi madalitso ochuluka. Lili ‘dalitso la Yehova limene limalemeretsa.’ (Miyambo 10:22) Ndipo chithandizo chake ndi dalitso nzimene zimatheketsa olengeza Ufumu ambiri kulimbikira mwachisangalalo muutumiki waupainiya.