Madalitso a Utumiki wa Upainiya
1, 2. Kodi ndi madalitso ati amene amapezeka pochita upainiya, ndipo n’chifukwa chiyani zili choncho?
1 Mpainiya wina anati: “Ndikudziŵa kuti palibe ntchito iliyonse imene ikanandithandiza kukhala wosangalala monga mmene kuuza ena choonadi kwandithandizira.” Mpainiya winanso anati: “Tsiku lililonse kukada, tulo tanga timakhala tabwino, ndipo ndimakhala ndi chimwemwe chachikulu.” Mmene apainiya ameneŵa akumvera ndi mmenenso amamvera abale ndi alongo amene alawa madalitso a upainiya kulikonse.—Miy. 10:22.
2 Kuthandiza ena kudziŵa zinthu za m’Mawu a Mulungu zimene zingapulumutse moyo wawo kumasangalatsa kwambiri. (Mac. 20:35; 1 Ates. 2:19, 20) Mpainiya wina amene watumikira kwa nthaŵi yaitali analemba kuti: “Zimasangalatsa ndiponso zimalimbitsa chikhulupiriro kuona mmene mphamvu ya Mawu a Mulungu imalimbikitsira anthu kusintha moyo wawo.” Inde, mwa kukhala okonzeka kuthandiza anthu ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo, apainiya amapeza madalitso ngati ameneŵa.
3, 4. Kodi kuchita upainiya kumaphunzitsa bwanji munthu kudalira Yehova, ndipo zimenezi zimamuthandiza bwanji kuti akule mwauzimu?
3 Kudalira Yehova: Kudalira mzimu wa Mulungu tsiku ndi tsiku pamene akuchita utumiki wawo kumathandiza apainiya kukhala ndi “chipatso cha Mzimu” ndipo zimenezi zimawateteza. (Agal. 5:16, 22, 23) Kuwonjezeranso pamenepo, popeza apainiya amagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu nthaŵi zonse, nthaŵi zambiri amadziŵa bwino kwambiri kugwiritsa ntchito Malemba poikira kumbuyo choonadi ndiponso polimbikitsa ena. (2 Tim. 2:15) Mbale wina amene wachita upainiya kwa zaka zambiri anati: “Upainiya wandithandiza kudziŵa zinthu zakuya za m’Baibulo, zimene ndazigwiritsa ntchito kuthandiza anthu ambiri kuti adziŵe Yehova ndi zolinga zake.” N’zopindulitsatu kwambiri zimenezi!
4 Apainiya okhazikika ayeneranso kudalira Yehova m’njira zina zambiri. Chikhulupiriro chawo chimalimba pamene aona mmene Yehova amadalitsira kuyesetsa kwawo kuti apeze zinthu zofunika pamoyo. Mpainiya wina wokhazikika wa zaka 72 amene wachita upainiya kwa zaka 55 anati: “Yehova sanandikhumudwitsepo.” Ndiponso, mwa kusafuna zinthu zambiri pa moyo wawo, apainiya amadziteteza ku nkhaŵa zambiri za m’moyo. Kodi zimenezi sizikukulimbikitsani?—Mat. 6:22; Aheb. 13:5, 6.
5. Kodi kuchita upainiya kumamuthandiza bwanji munthu kuyandikira kwa Yehova?
5 Kuyandikira kwa Mulungu: Ubwenzi wathu ndi Yehova ndicho chinthu chabwino kwambiri chimene tingakhale nacho pa moyo wathu. (Sal. 63:3) Tikamachita nawo utumiki mokwanira chifukwa chokonda Yehova, ubwenzi umenewo umakula. (Yak. 4:8) Mpainiya wina amene anachita utumikiwu kwa zaka 18 anati: “Upainiya umatithandiza ‘kulawa ndi kuona kuti Yehova ndiye wabwino,’ ndipo tsiku lililonse timakulitsa kwambiri ubwenzi ndi Mlengi wathu.”—Sal. 34:8.
6. Kodi apainiya ayenera kukhala ndi chiyani, ndipo ndaninso ena amene amapindula kupatulapo apainiyawo?
6 Kuwonjezera pa kukhala ndi mpata pa moyo wawo kuti achite utumikiwu, apainiya ayenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba, kukonda kwambiri Mulungu ndi anthu anzawo, ndiponso kufunitsitsa kudzimana. (Mat. 16:24; 17:20; 22:37-39) Komabe, monga mmene kusangalala kwa apainiya m’madera onse kukusonyezera, madalitso a upainiya ndi ochuluka kuposa kudzimana kumene amachita. (Mal. 3:10) Amene amapeza madalitso ameneŵa si apainiya okhawo. Mabanja awo ndiponso mpingo wonse umapindula ndi mtima wabwino umene apainiyawo amasonyeza.—Afil. 4:23.