Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/99 tsamba 3-4
  • Upainiya—Kugwiritsa Ntchito Nthaŵi Yathu Mwanzeru!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Upainiya—Kugwiritsa Ntchito Nthaŵi Yathu Mwanzeru!
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Apainiya Othandiza 3,000 Akufunika
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Madalitso a Utumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Madalitso a Utumiki wa Upainiya
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Cholinga Chabwino Kwambiri M’chaka Chautumiki Chatsopano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 4/99 tsamba 3-4

Upainiya—Kugwiritsa Ntchito Nthaŵi Yathu Mwanzeru!

1 ‘Pajatu ndine wotanganidwa kwambiri! Kodi kungakhale kwanzeru kuyamba upainiya panopo?’ Anaganiza motero mlongo wina pamene ankamvetsera nkhani yakuti “Kupitabe Patsogolo ndi Utumiki Waupainiya” yokambidwa pamsonkhano wadera ndi mkulu amenenso ali mpainiya. Mbale wachinyamata pagulu lomwelo anaganiza chonchi, ‘Kodi iwo amatha bwanji kuchita upainiya? Sindine mkulu, komatu ndili ndi zochita zochuluka!’

2 Pamene mkuluyo anapitiriza kufotokoza madalitso a upainiya, anafunsa apainiya angapo a m’deralo amene anasimba za masinthidwe amene iwo anapanga kuti achite upainiya komanso mmene Yehova anadalitsira khama lawo. Wina anali wolemala, wina wokhala ndi mnzake wa muukwati wosakhulupirira, ndipo winanso anasiya ntchito koma anatha kupeza zofunika. Atamva mmene apainiya ameneŵa anali kuchitira bwino mothandizidwa ndi Yehova, mbale ndi mlongo m’gulumo anayamba kupenda maganizo awo komanso mikhalidwe yawo. Tikukupemphani kuti inunso muchite zofananazo, makamaka poona kuti maola ofunika kwa apainiya achepetsedwa ndipo ofalitsa uthenga wabwino ambiri atha kukwanitsa maolawo tsopano.

3 Tikudziŵa kuti Yehova ndiye Mlengi komanso Mfumu ya Chilengedwe Chonse ndi kuti tili ndi moyo chifukwa cha iye. (Dan. 4:17; Mac. 17:28) N’zoonekeratu kwa ife kuti Yehova akugwiritsa ntchito gulu limodzi lokha. Tili ndi mwayi wotumikira ndi gululi mokhulupirika, kuchirikiza “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” pochitira umboni Ufumu mapeto asanadze. (Mat. 24:45; 25:40; 1 Pet. 2:9) Pokhala tili m’kati mwenimweni mwa “masiku otsiriza,” tikudziŵa kuti nthaŵi yoti tilalikire ikutha. (2 Tim. 3:1) Komanso, tifunikira kusamalira zosoŵa zakuthupi za mabanja athu. (1 Tim. 5:8) Malipiro a munthu salinso ochuluka monga kale. Mwinanso thanzi lathu silili bwino monga muja linalili kale. Ndipo kunena zoona, tifunikira nthaŵi ndi ndalama zoti tigwiritse ntchito. (Mlal. 3:12, 13) Ndiye tingadabwe ngati kulabadira pempho lakuti tichite upainiya kulidi kwanzeru.

4 Aliyense payekha afunika kupenda mikhalidwe mosamalitsa ndi kusankha kuchita upainiya kapena kusachita. (Aroma 14:12; Agal. 6:5) N’zosangalatsa kuona kuchuluka kwa amene alabadira pempho la kuchita upainiya. Mosasamala kanthu za mavuto ndi zothetsa nzeru za masiku ano otsiriza, lipoti la utumiki lofalitsidwa mu 1999 Yearbook likusonyeza kuti anthu a Yehova okwanira pafupifupi 700,000 kuzungulira dziko lonse akupitirizabe utumiki waupainiya. Kaya kumene akutumikirako kuli mavuto a zachuma, kayendedwe, kaya thanzi lawo silili bwino, kapenanso akukumana ndi mavuto osiyanasiyana, abale ndi alongo ameneŵa sakulema kuchita zabwino, ndipo zimenezi n’zoyamikirika. (Agal. 6:9) Iwo amuyesa Yehova mwa kuchita zimene iye amafuna. (Mal. 3:10) Iwo akuona kuti upainiya ndiwo njira yanzeru yogwiritsira ntchito nthaŵi yochepa imene ali nayo ndi chuma chawo ndipo Yehova wawadalitsa zedi chifukwa cha masinthidwe ofunikira omwe apanga kuti ayambe komanso kupitiriza ntchito yaupainiya.

5 Apainiya Akudalitsidwa: Mlongo wina ku Cameroon amene ali ndi mwana wamkazi wamng’ono kwambiri akufotokoza kuti: “Chibadwireni, mwana wanga wamkazi wakhala akutsagana nane mu utumiki. Ngakhale asanayambe n’kuyenda komwe, ndinkam’bereka. Tsiku lina mmaŵa tili mu utumiki, ndinaima pakasitolo kam’mbali mwa njira. Mwana wangayo anandisiya atanyamula magazini angapo omwe anatenga m’chikwama changa. Anayenda dzandidzandi kupita pakasitolo kotsatira. Ngakhale sakananena zambiri, anachititsa chidwi mayi wina ndipo anam’gaŵira magazini. Mayiyo anazizwa kuona mwana wamng’ono ngati ameneyu akuchita ntchito imeneyi. Analandira magaziniwo komanso analola phunziro la Baibulo la panyumba!”

6 Mkulu wina amenenso ndi mutu wa banja ku Zambia ndipo amagwira ntchito yolembedwa anasankha kuchita upainiya wothandiza atamva pempho lakuti pakufunika apainiya othandiza ambiri. Anachita zimenezi ngakhale kuti ali wotanganidwa kwambiri. Anafuna kupereka chitsanzo ku mpingo komanso ku banja lake. Nthaŵi zina, ankaimika galimoto lake m’mbali mwa msewu ndi kuikapo matepi a The Secret of Family Happiness ndi kuitana odutsa m’njira kuti adzamvetsere zimene zinali kuŵerengedwa mokwezazo. M’njira imeneyo, anagaŵira mabuku 16 a Chimwemwe cha Banja ndi mabuku 13 a Chidziŵitso, ndipo anayambitsa maphunziro a Baibulo aŵiri.

7 Mzimu wabwino waupainiya unaonekeranso m’dziko loyandikana nalo la Zimbabwe. M’mwezi wa April 1998, mpingo wina wa ofalitsa 117 unapereka lipoti la apainiya othandiza 70 ndi okhazikika 9. Mpingo winanso wa ofalitsa 94 unali ndi apainiya othandiza 58 amene anapereka lipoti. Komanso wina wa ofalitsa 126 unapereka lipoti losonyeza kuti 58 anasankha kuchita upainiya wothandiza limodzi ndi apainiya okhazikika 4. Chaka cha utumiki chapita chinali chapadera kwambiri m’Zimbabwe. Ngakhale kuti abale kumeneko anali otanganidwa kwambiri ndi mabanja, ntchito za mpingo, ndi kumanga nthambi, anayesetsa kugwiritsa ntchito mwanzeru nthaŵi yawo mu utumiki.

8 Apainiya amazindikira kuti kuyamba ntchito yaupainiya ndi kupitiriza sikudalira nyonga yawo. Sazengereza kuvomereza kuti zilizonse zimene amachita zimatheka chifukwa ‘amazichita mu mphamvu imene Mulungu awapatsa.’ (1 Pet. 4:11) Chikhulupiriro chawo chimawathandiza kuchita utumiki wawo tsiku ndi tsiku. M’malo mofunafuna ubwino wawo ndi zosangalatsa, apainiya achipambano amazindikira kuti m’pofunikira ‘kulimbikira kwambiri’ kuti apitirize, ndiponso amalandira madalitso ambiri.—1 Ates. 2:2, NW.

9 Chitsanzo cha Paulo n’Chofunika Kuchitsatira: Baibulo limasimba zimene mtumwi Paulo anachita mu utumiki ndi thandizo limene anapereka kwa anthu ambiri. Komanso, ngati panali munthu amene anali wotanganidwa anali Paulo. Anapirira chizunzo ndi mavuto ena kuti alalikire uthenga wabwino ndi kulimbitsa mipingo. Anapiriranso matenda osautsa kwambiri. (2 Akor. 11:21-29; 12:7-10) Anatsimikiza mtima kugwiritsa ntchito mwanzeru nthaŵi yake. Anavomereza kuti anachita ntchito yake yonse mothandizidwa ndi Yehova. (Afil. 4:13) Mwa anthu amene Paulo anawathandiza panalibe wonena kuti Paulo anangotaya nthaŵi ndi khama lake pachabe mu utumiki wa Yehova kapena kuti mwina akanachitapo bwino kusiyana ndi mmene anachitira. Inde, tikupindulabe ndi njira yanzeru imene Paulo anagwiritsira ntchito nthaŵi yake! Timayamikiratu uphungu wake wouziridwa wotithandiza kuonetsetsa zinthu zofunika ndi kumamatira choonadi nthaŵi zino zovuta.

10 Panopo kuposa ndi kalelonse, ‘yafupika nthaŵi yolalikira uthenga wabwino.’ (1 Akor. 7:29; Mat. 24:14) Ndiye chifukwa chake, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Moyo wanga utati uthe mwadzidzidzi, kodi ndingamuuze Yehova lero kuti ndagwiritsa ntchito nthaŵi yanga mwanzeru?’ (Yak. 4:14) Bwanji osalankhula ndi Yehova m’pemphero tsopano, ndi kumuuza za chikhumbo chanu chakuti mugwiritse ntchito nthaŵi yanu mwanzeru monga mmodzi wa Mboni zake? (Sal. 90:12) Pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni kupeputsa moyo wanu. Ngakhale ngati m’mbuyomu munkaona kuti simungathe kuchita upainiya, kodi panopo zingakhale kuti mutha kuuwonjeza pa moyo wanu?

11 Gwiritsani Ntchito Mkhalidwe Wanu Bwino Lomwe: Kunena zoona, sikuti onse ofunitsitsa kutumikira monga apainiya okhazikika atha kupatula maola 70 pamwezi. Mkhalidwe wawo suwalola. Komabe, ofalitsa ambiri amalinganiza zinthu kuti kaŵirikaŵiri kapena mopitiriza azipatula maola 50 pamwezi mu utumiki monga apainiya othandiza. Ngati mkhalidwe wanu panopo sukulolani kuchita upainiya wothandiza kapena wokhazikika, musataye mtima. Pitirizani kupemphera kuti mkhalidwe wanu usinthe. Ngati pakali pano n’kosatheka kupanga masinthidwe, khazikani mtima pansi podziŵa kuti Yehova amasangalala ndi chilichonse chimene muli wokhoza kuchita ndi moyo wonse mu utumiki wake. (Mat. 13:23) Amaona kuti mwaima zolimba kumbali yake ndi kuti mukuyesetsa kukhala wofalitsa wokhulupirika amene salola mwezi kudutsa popanda kupeza mpata wochitira umboni. Mwinamwake mutha kupita patsogolo mwa kunola maluso anu ochitira umboni, mukumalimbikira kuti mupambane monga mlaliki ndi mphunzitsi wa uthenga wabwino.—1 Tim. 4:16.

12 Pokhala kuti “tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa” layandikira kwambiri, tifunikira kugwiritsa ntchito mwanzeru nthaŵi yotsalayi kuti timalize ntchito imene tapatsidwa kuchita. (Yow. 2:31) Satana akudziŵa kuti nthaŵi yake yam’chepera, choncho kusiyana ndi kalelonse akuchita zonse zomwe angathe kutanganitsa moyo wathu ndi kutivutitsira zinthu kuti tisaike mtima wathu pa zinthu zofunikadi. (Afil. 1:10; Chiv. 12:12) Musachepetse chidwi chimene Mulungu ali nacho mwa inuyo. Yehova angakuthandizeni kupeputsa moyo wanu ndi kuchita zomwe mungathe mu utumiki. (Sal. 145:16) Chosangalatsa n’chakuti ambiri atapendanso mkhalidwe wawo, akupeza kuti atha kuloŵa pa mzera wa apainiya othandiza kapena okhazikika. Indedi, apainiya amakhutira kwambiri pogwiritsa ntchito mwanzeru nthaŵi yawo. Kodi inu mudzakhala mmodzi wa iwo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena