Apainiya Amapereka ndi Kulandira Madalitso
“UPAINIYA ngwamtengo wapatali kwambiri kuposa ntchito yachipambano yakudziko. Palibe chimene chimakhutiritsa kwambiri kuposa kuthandiza anthu kufika pakudziŵa Yehova ndi chowonadi chake.” Anatero mkazi wina Wachikristu amene anasankha upainiya—kulalikira Ufumu kwanthaŵi yonse—monga ntchito yake. Kodi ndintchito zina zingati zimene zingadzetse chimwemwe chotero?
Upainiya uli ponse paŵiri chonulirapo chapamwamba ndi mwaŵi wamtengo wapatali. Kodi ndimotani mmene munthu angasankhire moyo wotero? Kodi nchiyani chimene chikufunikira kuti munthu amamatire pa upainiya kwanthaŵi yaitali yomkhozetsa kupeza madalitso amene umapereka?
Zinthu ziŵiri nzofunika. Choyamba, mikhalidwe yabwino. Ambiri ali m’mikhalidwe imene mwachionekere simatheketsa upainiya. Ndipo chachiŵiri, ziyeneretso zauzimu ndi mkhalidwe wamaganizo woyenera. Ndithudi, kaya mikhalidwe yomwe ilipo imalola munthu kuchita upainiya kapena ayi, onse angalimbikire pa kukulitsa mikhalidwe yauchikulire Yachikristu.
Chifukwa Chake Ena Amachita Upainiya
Kodi ziyeneretso za upainiya wachipambano nzotani? Eya, maluso a kulalikira ali ofunika kwambiri. Apainiya afunikira kudziŵa mmene angaperekere mbiri yabwino kwa anthu amene sawadziŵa, kuchita maulendo obwereza pa okondwerera, ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Kusoŵeka kwa maluso ameneŵa kungalefule mpainiya. Komabe, zinthu zina nzofunikanso.
Mwachitsanzo, zilizonse zokhudza kulambira kwathu zili zogwirizana ndi unansi wathu ndi Yehova ndi gulu lake. Zimenezi zimaphatikizapo upainiya. Mpainiya wachichepere wotchedwa Rado anafotokoza kuti: “Kwa munthu wachichepere, palibe kanthu kabwino koposa kukumbukira Yehova ndi kuyenda m’njira ya chowonadi.” Inde, upainiya uli njira yabwino kwa achichepere yosonyezera chikondi chawo pa Yehova ndi kuyandikana naye kwawo.—Mlaliki 12:1.
Chidziŵitso ndi kuzindikira zilinso zofunika kwambiri. (Afilipi 1:9-11) Kwenikweni, zimenezi ndizo mafuta amene amachititsa injini yathu yauzimu kugwira ntchito. Phunziro laumwini lokhazikika nlofunika kuti tipeŵe kukhala ofooka mwauzimu, tikumatayikiridwa ndi changu chathu ndi chikhulupiriro. Ndithudi, chidziŵitso chimene timapeza chiyenera kuyambukira osati nzeru zokha komanso ndi mtima. (Miyambo 2:2) Chotero, kuwonjezera pa phunziro laumwini, tifunikira nthaŵi ya kupemphera ndi kusinkhasinkha kotero kuti chidziŵitso chimene timapeza chikhudze mtima. Ndiyeno, ngati mikhalidwe yathu ilola, tidzafuna kuchita upainiya.—Yerekezerani ndi Ezara 7:10.
Kuyamba utumiki waupainiya kumafunanso mzimu wa kudzimana. Mnyamata wina wotchedwa Ron anapanga makonzedwe ake onse a kuchita upainiya. Anali kungoyembekezera mikhalidwe yoyenera kuti ayambe kutero. Kwenikweni, anali kufuna ntchito imene ikamlola kuchita upainiya ndipo panthaŵi imodzimodzi kupeza zina za zinthu zabwino zosangulutsa kwambiri m’moyo. Pamene anauza mlongo wachikulire zimenezi, yankho lake linamdabwitsa. Mlongoyo anati: “Yehova amadalitsa zochita, osati malonjezo.” Mnyamatayo anapeza ntchito ya malipiro ochepa imene inampatsa nthaŵi yochita upainiya. Kugwiritsira ntchito Mateyu 6:25-34 kudzathandiza munthu kupeza bwino ndi ndalama zochepa.
Kufunitsitsa kodzichepetsa kutsatira malingaliro abwino operekedwa kungatithandizedi kuloŵa muutumiki waupainiya. Atangokhala Mkristu, Hanna anakulitsa chikhumbo cha kuchita upainiya. Koma sanachite upainiya pamene anali kusamalira banja, ndipo pambuyo pake anayamba ntchito yabizinesi. Polabadira uphungu wabwino wa akulu atcheru, iye anasiya ntchito yake yakudziko yosangalatsayo nayamba utumiki waupainiya. Tsopano Hanna amapeza chisangalalo chachikulu mwa kufikitsa ena kukudzipatulira ndi kuthandiza ofooka.
Kuyamikira zimene chowonadi chachita m’moyo wa munthu kungakhalenso mphamvu yosonkhezera kuchita upainiya. Talingalirani nkhani ya mkazi wina wochita tondovi kwambiri amene ukwati wake unali kusweka. Mkhalidwe umenewu unasintha mwadzidzidzi pamene anaphunzira chowonadi cha Mawu a Mulungu ndi kuchigwiritsira ntchito. Pokhala wokondwera ndi zimene chowonadi chinamchitira, anaganiza kuti njira yake yabwino koposa yosonyezera chiyamikiro ikakhala kuchita upainiya ndi kuthandiza ena. Anachita zimenezo, ndipo tsopano amapeza madalitso a maphunziro ambiri a Baibulo ndi moyo wabanja wachimwemwe.
Ena Angathandize
Kaŵirikaŵiri apainiya amatulutsa apainiya ena. Rado, wotchulidwa poyamba, anali wazaka zisanu ndi chimodzi pamene apainiya aŵiri anaphunzira Baibulo ndi makolo ake. Adakali wamng’ono kwambiri, iye nthaŵi zonse anatsagana ndi alengezi anthaŵi yonse ameneŵa muutumiki wakumunda. Rado mwiniyo anakhala mpainiya wokhazikika pausinkhu wazaka 17. Mnyamata wina, Arno, analeredwera m’banja Lachikristu koma anakhala wofooka mwauzimu. Pambuyo pake, anayambiranso kubwezeretsa nyonga yake yauzimu, ndipo tsopano akuti: “Ndinalandira chilimbikitso chachikulu kwa apainiya. Ndinayanjana nawo makamaka pamatchuthi a sukulu ndipo nthaŵi zina ndinapereka lipoti la utumiki wakumunda la maola 60 pamwezi. Pambuyo pa zimenezo, kuloŵa pakhomo la utumiki waupainiya wokhazikika [wofuna maola 90 pamwezi] kunali kosavuta kwambiri.” Kusinkhasinkha uphungu wa pa 1 Akorinto 7:29-31 wa kusachititsa nalo dziko kwathandizadi achichepere otero.
Mzimu waupainiya ungazike mizu mosavuta m’banja mmene zinthu zauzimu zili ndi malo oyamba ndi kumene makolo amalimbikitsa ana awo kuloŵa muutumiki wanthaŵi yonse. Philo, amene anakulira m’banja lotero, akuti: “Ambiri anandiuza kupitiriza ndi maphunziro anga, kugwirira ntchito mtsogolo mwakudziko. Koma makolo anga anandithandiza kupanga chosankha chanzeru. Anandiuza kuti ngati ndinafunadi kukonzekera za mtsogolo, chinthu changa choyamba chinayenera kukhala kukulitsa unansi ndi Yehova.”
Mtsikana wina wotchedwa Thamar nayenso akunena kuti chitsanzo ndi zoyesayesa za makolo ake ndizo zinamchititsa kuyamba utumiki waupainiya. Iye akuti: “Sindingathe kwenikweni kunena pamene ndinakulitsa lingaliro lauzimu la moyo, koma ndidziŵa kuti sindinabadwe nalo. Chizoloŵezi cha makolo anga cha kupita nthaŵi zonse muutumiki wakumunda ndi kupezeka pamisonkhano, limodzinso ndi chikondi chawo chakuya cha chowonadi, zinandithandiza kwambiri kukulitsa kapenyedwe kanga ka zinthu kauzimu.”
Kumamatira ku Chosankha Chanu
Munthu atayamba utumiki waupainiya, kuchita khama kumamtheketsa kututa mapindu onse a chosankha chanzeru chimenecho. Uphungu wothandiza wochuluka pa zimenezo ungaperekedwe. Mwachitsanzo, apainiya angachite bwino kuphunzira mmene angalinganizire nthaŵi yawo kuichititsa kukhala yopindulitsa kwambiri monga momwe kungathekere. Komabe, mbali yofunika koposa imapitirizabe kukhala unansi wa munthuyo ndi Yehova ndi gulu Lake.
Chogwirizana ndi zimenezo ndicho mkhalidwe wa maganizo wapemphero. “Pamene ndinabwera m’chowonadi, ndinafuna kwambiri kuchita upainiya,” akutero Cor. Komabe, atate wake anafuna kuti choyamba amalize kosi pa Agricultural University. Pambuyo pake, Cor anayamba upainiya. M’kupita kwa nthaŵi anakwatira, ndipo mkazi wake anagwirizana naye m’ntchito yaupainiya. Pamene mkazi wake anakhala ndi pathupi, iye anaona kuthekera kwa kusiya ntchito yaupainiya. “Ndinapemphera kaŵirikaŵiri kwa Yehova ndi kumuuza chikhumbo changa chochokera mumtima cha kupitiriza upainiya,” akutero Cor. M’kupita kwa nthaŵi Cor anapeza ntchito imene inamtheketsa kuchita upainiya pamene anali kusamalira banja.
Kukhala wokhutira ndi zinthu zofunika zakuthupi ndiko chinthu china chimene kaŵirikaŵiri chimathandiza munthu kupitiriza muutumiki waupainiya. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5) Kukhala wokhutira ndi zinthu zomwe zilipo kunathandiza Harry ndi Irene kupitiriza upainiya. Irene, amene ali wakhungu, wakhala mpainiya kwa zaka zisanu ndi zitatu. “Mkhalidwe wathu wa zandalama sitinauone monga vuto konse,” iye akutero. “Tinangosamala kuti tisadzitengere mtolo wosafunikira wa zandalama. Nthaŵi zonse taŵerengera mtengo. Miyoyo yathu yakhala yachikatikati nthaŵi zonse, koma yosangalatsa kwambiri, ndipo yakhala yodzaza ndi madalitso.”
Chisangalalo ndi Madalitso Ochuluka
Poyang’ana kumbuyo pa zaka zoposa zisanu ndi zinayi za upainiya, Thamar akuti: “Umafikira pakuyandikana kwambiri ndi Yehova, ngati kuti wakugwiradi padzanja.” (Salmo 73:23) Ndiponso ziyeso zina zimakumbukika. “Kupanda ungwiro kwanga ndi kuja kwa ena kunandisautsa nthaŵi zonse,” akuwonjezera motero Thamar. “Ndiponso, ndinkayang’ana abale ndi alongo amene anasankha njira ya moyo yofupa kwambiri mwakuthupi, ndipo chosankha chawo chinaoneka kukhala chabwinopo pamene ndinali kupita kunyumba ndi nyumba mu mvula ndi m’chisanu. Koma mkati mwa mtima wanga, sindinafune kusinthanitsa malo. Kodi nchiyani china kusiyapo upainiya chimene chikanadzetsa chisangalalo chotero, chikhutiro chauzimu, ndi madalitso otero?” Kodi inu mungayamikire kwambiri chisangalalo ndi madalitso ofanana ndi zimenezo?
Chifukwa chakuti apainiya amathera nthaŵi yochuluka muutumiki Wachikristu, akhoza kuthandiza anthu ambiri kupeza chidziŵitso cha chowonadi cha Baibulo. Harry ndi Irene, amene atchulidwa papitapo, akuti: “Pali mwaŵi wochuluka umene ungapezedwe m’gulu la Yehova, koma kuthandiza wokondwerera chatsopano kupita patsogolo kufikira pa kukhala mtumiki wa Yehova ndiwo mwaŵi waukulu koposa.”
Mpainiya wina anafotokoza zinthu bwino pamene anati: “Mawu a pa Miyambo 10:22 akhaladi owona kwa ine: ‘Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.’ Nthaŵi zambiri, lemba limeneli lakwaniritsidwa pa ine m’zaka zimene ndatumikira Yehova.”
Makolo, kodi mukukhomereza mwa ana anu chikhumbo cha kuchita upainiya? Apainiya, kodi mumayesayesa kukulitsa chikhumbo chimenechi mwa ena? Akulu, kodi mumachirikiza apainiya mumpingo wanu ndi kuthandizira kukulitsa mzimu waupainiya mwa ena? Anthu owonjezerekawonjezereka a Yehova asonkhezeredwetu kukalimira madalitso ochuluka otero pamene achita utumiki waupainiya.