Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/98 tsamba 3-5
  • Utumiki Waupainiya—Kodi Ngoyenera Inu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Utumiki Waupainiya—Kodi Ngoyenera Inu?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Apainiya Amapereka ndi Kulandira Madalitso
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Madalitso a Utumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Upainiya Umalimbitsa Ubwenzi Wathu Ndi Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2013
  • “Upainiya Ungakuyenereni Kwabasi!”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 7/98 tsamba 3-5

Utumiki Waupainiya—Kodi Ngoyenera Inu?

1 “Sindikuganiza kuti ndingachitenso kanthu kena. Sindikuganiza kuti pali chinthu china chimene chingandisangalatsenso.” Kodi anatero ndani? Mmodzi mwa Mboni za Yehova zikwi zambiri zimene zikuchita utumiki wanthaŵi zonse monga ntchito yawo yosangalatsa pamoyo. Kodi mwaganizirapo mwa pemphero ngati utumiki waupainiya uli woyenera inu? Poti tinadzipereka ndi mtima wonse kwa Yehova, tiyeneradi kuganizira za kulimbikira kwambiri kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu. Ndi cholinga chimenecho, taganizirani mafunso ena okhudza upainiya amene ambiri amafunsa.

FUNSO 1: “Ena amati upainiya si wa aliyense. Ndiye ndingadziŵe bwanji ngati ndikuyenerera?”

2 Zimene zingayankhe funsolo ndizo mikhalidwe yanu ndiponso ntchito zina zimene Malemba amakulamulani kuchita. Pali ambiri amene thanzi lawo kapena mkhalidwe wawo m’moyo sumawalola kuwonongera maola 90 mwezi uliwonse mu utumiki. Mwachitsanzo talingalirani za alongo ambiri achikristu okhulupirika omwe ali pabanja ndipo ali ndi ana. Amagwira ntchito mu utumiki kaŵirikaŵiri monga mmene angathere, malinga ndi momwe mikhalidwe yawo ingawalolere. Mipata ikamapezeka, amachita upainiya wothandiza mwezi umodzi kapena ingapo chaka chilichonse, namapeza chimwemwe chimene chimadza mwa kuwonjezera ntchito yawo mu utumiki. (Agal. 6:9) Ngakhale kuti mikhalidwe yawo siingawalole kuchita upainiya wanthaŵi zonse pakali pano, amakulitsa mzimu waupainiya ndipo ali dalitso mumpingo chifukwa amalalikira uthenga wabwino mwachangu.

3 Komanso, abale ndi alongo ena amene sali omangika kwambiri amakwanitsa kuchita upainiya mwa kuuika pamalo oyamba a zochita zawo zonse. Nanga inuyo? Kodi ndinu wachinyamata yemwe wangotsiriza kumene sukulu yake yakudziko? Kodi ndinu mkazi amene mwamuna wake amakwanitsa kusamalira banja mosavuta? Kodi ndinu wokwatiwa (wokwatira) koma wopanda ana omwe amadalira thandizo lanu? Kodi mwapuma pantchito yolembedwa? Munthu aliyense angadzisankhire kaya kuchita upainiya kapena kusauchita. Funso nlakuti, Kodi mungapeze nthaŵi m’moyo wanu yochita upainiya? Ngati mungathe kusintha mikhalidwe yanu kuti mukhale mpainiya, bwanji osaisintha?

FUNSO 2: “Kodi ndingatsimikize bwanji kuti sindidzisoŵa ndalama mu utumiki wanthaŵi zonse?”

4 Nzoona kuti m’maiko ambiri maola ofunika pantchito yolembedwa mlungu uliwonse kuti munthu apeze zimene zili ngati zofunika pamoyo awonjezeka pakupita kwa zaka. Komabe, ambiri akhala akuchita upainiya kwa zaka makumi ambiri, ndipo Yehova akuwachirikizabe. Kuti zisakuvuteni monga mpainiya, mufunikira chikhulupiriro ndi mzimu wodzimana. (Mat. 17:20) Salmo 34:10 limatilonjeza kuti “iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.” Aliyense amene akuyamba utumiki waupainiya ayenera kutero ali ndi chidaliro ndithu kuti Yehova adzamsamala. Iye akusamala kumene apainiya okhulupirika kulikonse! (Sal. 37:25) Nzoona, malinga ndi mapulinsipulo a pa 2 Atesalonika 3:8, 10, ndi 1 Timoteo 5:8, apainiya samayembekezera ena kuwachirikiza ndi ndalama.

5 Aliyense amene akuganiza za utumiki waupainiya ayenera kuchita mmene Yesu ananenera: ‘Thangani mwakhala pansi, nimuŵerengere mtengo wake.’ (Luka 14:28) Imeneyo ndiyo nzeru yeniyeni. Chezani ndi amene zinawayendera bwino mu upainiya kwa zaka zambiri. Afunseni mmene Yehova akuwachirikizira. Woyang’anira dera lanu ali mpainiya wozoloŵera amene angakuuzeni njira zimene mungapambanire mu utumiki wanthaŵi zonse.

6 Dziko lotizingali likumka nalikonda chuma kwambiri. Likutisonkhezera kwambiri kuti tilitsanzire. Komabe, chifukwa cha kukonda utumiki wanthaŵi zonse, timadzichepetsa nkumakhutira ndi zimene tili nazo, ngakhale zichepe. (1 Tim. 6:8) Apainiya a moyo wosalira zambiri ndi wolongosoka ali ndi nthaŵi yambiri ya utumiki ndipo amapezadi chimwemwe ndi nyonga yauzimu pophunzitsa ena choonadi.

FUNSO 3: “Poti ine sindinakule, ndingamaganizirenji zosankha utumiki waupainiya monga ntchito?”

7 Potsiriza zaka zanu zomaliza kusukulu, nkwachibadwa kuganiza za tsogolo lanu. Mumafuna kuti likhale tsogolo lotsimikizika, labwino, limene mudzakhutira nalo. Aphungu a pasukulu angakusonkhezereni kupeza ntchito yandalama zambiri imene imafuna kuti muthe zaka zambiri kukoleji.

8 Zimene mungasankhe kuchita pakali pano m’moyo wanu nzimene zingasonyeze mmene tsogolo lanu lonse lidzakhalira. Ngati mwakhala kale Mboni ya Yehova yodzipereka, yobatizidwa, ndiye kuti mwadzipereka ndi mtima wonse kwa Yehova. (Aheb. 10:7) Mpata woyamba umene mungapeze, yesani upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi kapena ingapo. Mukatero mudzalaŵa chimwemwe ndi maudindo amene upainiya wokhazikika umabweretsa, ndipo chithunzi cha zimene mukufuna kuchita ndi moyo wanu chidzaoneka bwino mosakayikira. Ndiye, m’malo moti muyambe ntchito yolembedwa mutatsiriza sukulu, bwanji osayamba upainiya wokhazikika?

9 Poti ndinu wachinyamata, gwiritsirani ntchito bwino nthaŵi yanu kukhalabe mbeta kuti muone mapindu amene ntchito yolalikira nthaŵi zonse imabweretsa. Ngati mukufuna kudzakwatira tsiku lina, palibe maziko ena abwino a ukwati amene mungamange kuposa kuyamba mwatumikira m’ntchito yaupainiya. Mmene mukukhwima maganizo ndi mwauzimu, mungasankhe kuti upainiya ukhale ntchito yanu limodzi ndi mnzanu wamuukwati wokondanso upainiya. Amuna ena ndi akazi awo amene ankachitira upainiya limodzi aloŵa ntchito yadera kapena m’munda waumishonale. Palibe moyo wina wokhutiritsa kuposa umenewo!

10 Zilibe kanthu kuti mudzachita upainiyawo kwa utali wotani, komabe, mudzakhala mutatsiriza maphunziro anu, mutaphunzira zinthu zamtengo wapatali zimene simukanazipeza pantchito ina iliyonse padziko lapansi. Upainiya umamphunzitsa munthu kudzilanga, kulinganiza zinthu bwino, kudziŵa kukhala bwino ndi anthu, kudalira Yehova, ndi mmene angakulitsire kuleza mtima ndi chifundo—mikhalidwe imene idzamthandiza kusenza maudindo ena aakulu.

11 Moyo wa anthu wafikira pakukhala wokayikitsa zedi. Nzinthu zochepa chabe zimene zili zokhalitsa, kusiyapo zimene Yehova walonjeza. Popeza kuti tsogolo lanu likukudikirani, kodi ndi nthaŵi ina iti yabwino kuposa tsopano lino imene mungaganizire kwambiri zimene mudzachita ndi moyo wanu m’zaka zikudzazi? Tauganizirani mosamala mwayi waupainiya. Simudzachita chisoni kuti munasankha utumiki waupainiya monga ntchito yanu.

FUNSO 4: “Kodi sumachita kuvutikira nthaŵi zonse kukwanitsa maola ofunikawo? Nanga ntatsalira m’mbuyo zingakhale bwanji?”

12 Polemba fomu ya upainiya wokhazikika, muyenera kuyankha funso lakuti: ‘Kodi mwalinganiza zochita zanu kuti mudzakwanitse kufikitsa maola ofunikawo 1,000 pachaka?’ Kuti muwakwanitse, mufunikira kukwanitsa maola atatu patsiku mu utumiki. Mwachionekere, zimenezo zimafuna kukhala ndi ndandanda yabwino ndi kudzilanga. Apainiya ambiri amadzakhala ndi ndandanda yabwino, yotsatirika m’miyezi yoŵerengeka chabe.

13 Sikumatheka nthaŵi zonse kumlola munthu kukhalabe pampambo wa apainiya ngati mikhalidwe yake siikumlolanso kukwanitsa maola ofunikira. Komabe, Mlaliki 9:11 amanena zoona akamati: “Yense angoona zomgwera m’nthaŵi mwake.” Matenda aakulu ndi mikhalidwe ina yosayembekezera ingampangitse mpainiya kutsalira mmbuyo. Ngati vutolo lili la kanthaŵi chabe ndipo ngati lachitika kuchiyambi kwa chaka chautumiki, mwina mudzangofunikira kuchita machaŵi. Nanga bwanji ngati vutolo labuka kutangotsala miyezi yoŵerengeka kuti chaka chautumiki chithe, ndiye mpainiya nkulephera kukwanitsa?

14 Ngati mwadwala kwa kanthaŵi kapena ngati pabuka vuto lina ladzidzidzi loti simungalithetse, ndiyeno nkulephera kukwanitsa maola, mungafikire wina wa Komiti Yautumiki Yampingo, nkumfotokozera vutolo. Ngati akuluwo akuganiza kuti zingakhale bwino kukulolani kupitiriza mu utumiki waupainiya popanda kudera nkhaŵa ndi nthaŵi imene inatayikayo, angasankhe kukuuzani zimenezo. Mlembi adzalemba pakhadi la Cholembapo cha Wofalitsa cha Mpingo kusonyeza kuti simukufunikira kuikwanitsa nthaŵi yotayikayo. Chimenecho si tchuti, koma angokuganizirani mwapadera chifukwa cha mikhalidwe yanu.—Onani mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa August 1986, ndime 18, (Chingelezi).

15 Apainiya ozoloŵera amagwiriratu ntchito ya maola ambiri kuchiyambiyambi kwa chaka chautumiki. Utumiki wawo waupainiya ndiwo umakhala woyamba, choncho nthaŵi zina iwo amaona kuti nkofunika kunyalanyaza zinthu zosafunika. Ngati mpainiya watsalira mmbuyo chifukwa chosachita zinthu molongosoka kapena chifukwa chakusatha kudzilamulira kutsatira ndandanda yake, ayenera kuona kuti imeneyo ndi ntchito yake yoti akwanitse maola otayikawo koma asayembekezere kuganiziridwa mwapadera.

16 Tikukhulupirira kuti makonzedwe akulingalira mwapadera anthu okumana ndi mavuto adzalimbikitsa ambiri kulembetsa utumiki waupainiya popanda kudera nkhaŵa mosafunikira. Makonzedwewo adzalimbikitsanso amene ali kale mu utumiki wanthaŵi zonse kuchitabe upainiya. Tikufuna kuti zinthu ziziwayendera bwino apainiya mu utumiki wawo wanthaŵi zonse.

FUNSO 5: “Ndimafuna kuchita kanthu kena kamene kazindisangalatsa pokachita. Kodi utumiki waupainiya ungandikhutiritse?”

17 Chimwemwe chenicheni munthu amachipeza makamaka ngati ali paunansi waubwenzi ndi Yehova ndi kudziŵanso kuti akumtumikira mokhulupirika. Yesu anapirira mtengo wozunzirapo “chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake.” (Aheb. 12:2) Anapeza chimwemwe chifukwa ankachita chifuniro cha Mulungu. (Sal. 40:8) M’dongosolo la zinthu lilipoli, tingakhale ndi chimwemwe chenicheni ngati zochita zathu zambiri m’moyo wathu zili zogwirizana ndi kulambira Yehova. Kuchita zinthu zauzimu kumatipangitsa kuzindikira kuti tikuzichita ncholinga chabwino chifukwa mumtima mwathu timadziŵa kuti tikuchita zoyenera. Chimwemwe chimachokera m’kupatsa, ndipo palibenso njira ina yabwino yoposa yakudzipereka tokha pophunzitsa ena mmene angapezere moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu.—Mac. 20:35.

18 Choncho, nchiyani chimene chimakubweretserani chimwemwe? Ngati mumakonda ntchito yokhalitsa ndi yopindulitsa kuposa chimwemwe cha kanthaŵi chimene dzikoli lingakupatseni, upainiya udzakupatsani luso labwino lochitira zinthu ndipo muzapezadi chimwemwe chenicheni.

FUNSO 6: “Ngati si wofunika kuti munthu apeze moyo wosatha, kodi sizili kwa ine kudzisankhikira kuti ndichite upainiya kapena ayi?”

19 Nzoona, mumasankha nokha kuchita upainiya. Kokha Yehova ndiye angakuweruzeni pa mikhalidwe yanu m’moyo. (Aroma 14:4) Ayeneradi kukuyembekezerani kumtumikira ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, nzeru zanu zonse, ndi mphamvu yanu yonse. (Marko 12:30; Agal. 6:4, 5) Amakonda wopatsa mokondwera, yemwe amamtumikira mwachimwemwe, osati monyinyirika kapena mokakamizika. (2 Akor. 9:7; Akol. 3:23) Chifukwa chanu chochitira utumiki wanthaŵi zonse chiyenera kukhala chakuti mumakonda Yehova ndi anthu a m’dera lanu. (Mat. 9:36-38; Marko 12:30, 31) Ngati mumamva choncho, ndiye kuti utumiki waupainiya uganizireni kwambiri.

20 Pansipo pasindikizidwa kalenda yoti “Ndandanda Yanga ya Mlungu ndi Mlungu ya Utumiki Waupainiya.” Taonani ngati mungadzaze ndandanda yokuyenerani, imene ingakuloleni kukwanitsa maola 23 pamlungu mu utumiki. Ndiyeno, khulupirirani Yehova ndi kumdalira kwambiri. Angakuthandizeni kupambana! Analonjeza kuti: ‘Ndidzakutsanulirani mdalitso wakuti adzasoŵeka malo akuulandira.’—Mal. 3:10.

21 Ndiyeno tifunse choncho kuti, “Utumiki waupainiya—kodi ngoyenera inu?” Ngati munganene kuti “Inde,” sankhani deti lodzayamba msanga upainiya wokhazikika, ndipo dziŵani kuti Yehova adzakudalitsani ndi moyo wosangalatsa!

[Tchati patsamba 5]

(Onani mu Utumiki wa Ufumu kuti mumvetse izi)

Ndandanda Yanga ya Mlungu ndi Mlungu ya Utumiki Waupainiya

LOLEMBA: Mmaŵa utumiki wakumunda

LACHIŴIRI: Mmaŵa utumiki wakumunda

LACHITATU: Mmaŵa utumiki wakumunda

LACHINAYI: Mmaŵa utumiki wakumunda

LACHISANU: Mmaŵa utumiki wakumunda

LOŴERUKA: Mmaŵa utumiki wakumunda

LAMLUNGU: Mmaŵa utumiki wakumunda

LOLEMBA: Masana utumiki wakumunda

LACHIŴIRI: Masana utumiki wakumunda

LACHITATU: Masana utumiki wakumunda

LACHINAYI: Masana utumiki wakumunda

LACHISANU: Masana utumiki wakumunda

LOŴERUKA: Masana utumiki wakumunda

LAMLUNGU: Masana utumiki wakumunda

LOLEMBA: Madzulo utumiki wakumunda

LACHIŴIRI: Madzulo utumiki wakumunda

LACHITATU: Madzulo utumiki wakumunda

LACHINAYI: Madzulo utumiki wakumunda

LACHISANU: Madzulo utumiki wakumunda

LOŴERUKA: Madzulo utumiki wakumunda

LAMLUNGU: Madzulo utumiki wakumunda

Gwiritsirani ntchito pensulo kulemba zochita zanu za tsiku ndi tsiku pamlungu.

Konzani ndandanda imene ingakuloleni kukwanitsa maola ngati 23 mlungu uliwonse mu utumiki wakumunda. Maola onse pamlungu ____________________

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena