Mbali ya Mafunso
◼ Kodi nchiyani chimene mlembi ayenera kuchita pamene mpainiya wokhazikika asamukira mu mpingo?
Mlembi ayenera kudziŵitsa Sosaite, akumagwiritsira ntchito danga losonyezedwa kutseri kwa Lipoti la Mpingo (S-1). Ayeneranso nthaŵi yomweyo kulembera mlembi wa womwe unali mpingo wakale wa mpainiyayo ndi kupempha makhadi onse a Cholembapo cha Wofalitsa cha Mpingo (S-21) amene ali mu faelo limodzinso ndi kalata yomdziŵikitsa yochokera ku Komiti Yautumiki Yampingo.
Pamene mpainiya asamukiratu, kaŵirikaŵiri amakhala ndi mavuto a kukhazikika ndi kukhazikitsa zizoloŵezi zabwino za utumiki. Mpainiya amayamikira kwambiri pamene akulu apereka chithandizo chachikondi kwa iye kotero kuti kusamukira kwake mu mpingo watsopano kukhale kopanda mavuto monga momwe kungathekere.
Chikumbutso: Mlembi amagaŵira makhadi ena a Pioneer Service Identification (S-202) kokha kwa apainiya a mommuno mu Malaŵi amene asamukira mu mpingowo. Apainiya amene ataya khadi lawo, amene asintha dzina lawo chifukwa cha ukwati kapena chisudzulo, ndi zina zotero ayenera kulandira makhadi awo atsopano kuchokera ku Sosaite, osati kwa mlembi. Mlembi kapena mpainiyayo ayenera kulembera Sosaite, akumalongosola za mkhalidwewo, ndi kupempha khadi latsopano.