Zinthu Zotithandiza Kuti Tipeŵe Magazi
Ofalitsa obatizidwa omwe m’mbuyomu analemba khadi la Chidziŵitso kwa Madokotala/Chowamasula ku Mlandu kapena Khadi la Mwana afunika kulemba makadi atsopano chaka chino. Pa Msonkhano wa Utumiki wa mlungu woyambira December 29, mlembi akhale ndi makadi okwanira ofalitsa obatizidwa ndi ana awo. Ngati mpingo ulibe makadi okwanira, mlembi angafufuze ku mipingo yomwe wayandikana nayo kapena aitanitse makadi ena mpingo ukamaitanitsa mabuku paulendo wotsatira.
Makadiŵa akalembedwere kunyumba bwinobwino koma OSASAINA. Makadiŵa adzasainidwe, kuchitira umboni, ndiponso kulemba deti pa Phunziro la Buku la Mpingo lotsatira, ndipo woyang’anira phunziro la bukulo angathandize amene akufuna thandizo. Anthu ochitira umboni afunika kuona mwini khadilo akulisaina.
Ofalitsa osabatizidwa angadzilembere makadi awo ndiponso a ana awo mwa kukopera zomwe zili pa khadi la Chidziŵitso kwa Madokotala/Chowamasula ku Mlandu ndi pa Khadi la Mwana.