Kodi Mumanyalanyaza?
Kunyalanyaza kuchita chiyani? Kulemba khadi la DPA (Khadi Lopatsa Munthu Mphamvu Yosasinthika Yondisankhira Thandizo la Mankhwala) limene Mboni zobatizidwa zimafunika kukhala nalo. Palibe ‘amene amadziwa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.’ Choncho, m’pofunika kusankhiratu chithandizo chamankhwala chimene mungalandire patachitika ngozi ndi kulemba zimene mwasankhazo. (Yak. 4:14; Mac. 15:28, 29) Kuti mumve zambiri pa nkhaniyi, werengani bwinobwino mutu 7 wa buku la “Chikondi cha Mulungu” ndi malifalensi amene asonyezedwa mmenemo. Kenako pambuyo popemphera gwiritsani ntchito mafunso ali m’munsiwa kubwereza zimene mwaphunzira.
(1) Kodi Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti chiyani pa nkhani yoika munthu magazi athunthu ndi zigawo zikuluzikulu za magazi? (2) Kodi pa nkhani ya magazi, Akhristu angasankhe mosiyana pa mbali ziti? (3) Kodi nkhani zokhudza chikumbumtima tiyenera kuziona bwanji? (4) Kodi munthu angakumane ndi mavuto otani m’thupi lake ngati waikidwa magazi? (5) Kodi pali njira zotani zimene zikugwiritsidwa ntchito kuchepetsa vuto lotaya magazi popanga opaleshoni? (6) Kodi ana aang’ono kapena anthu ena amene moyo wawo uli pangozi, angapatsidwe chithandizo chamankhwala popanda kuwaika magazi? (7) N’chifukwa chiyani Mkhristu ayenera kusankhiratu chithandizo chamankhwala chosagwiritsa ntchito magazi? Kodi tingachite motani zimenezi?
Kuvomera kapena kukana chithandizo chamankhwala chotchulidwa m’buku la “Chikondi cha Mulungu,” ndi chosankha cha munthu aliyense payekha mogwirizana ndi chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo. Kodi mwasankha chithandizo chamankhwala chenicheni chimene inu ndi ana anu mungalandire ndipo kodi mwalemba zimenezi pakhadi? Onani nkhani yakuti “Kodi Ndimaiona Bwanji Nkhani Yokhudza Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zachipatala Zogwiritsa Ntchito Magazi Anga Omwe,” m’mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2006. Pomaliza onetsetsani kuti mwalemba bwinobwino zinthu zimene mwasankha pakhadi lanu la DPA. Zinthu zimene mwasankhazo muyenera kudziwitsa munthu wokuimirani pa chithandizo chamankhwala ndiponso achibale anu onse omwe si Mboni.
[Bokosi patsamba 3]
• Kodi mwasankha chithandizo ndiponso njira zachipatala zimene inuyo ndi ana anu mungalole?
• Kodi mumatenga khadi lanu la DPA lolembedwa bwinobwino kuti likuthandizeni ngati mutachita ngozi?