Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/12 tsamba 3
  • Kodi Mwakonzekera Ngati Mutachita Ngozi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mwakonzekera Ngati Mutachita Ngozi?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mumanyalanyaza?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Kodi Mumanyalanyaza?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
km 1/12 tsamba 3

Kodi Mwakonzekera Ngati Mutachita Ngozi?

Tonsefe tikhoza kuchita ngozi mwadzidzidzi. (Yak. 4:14) Choncho, munthu wochenjera amachita zonse zimene angathe kuti akonzekere. (Miy. 22:3) Kodi munasankha kale chithandizo chamankhwala ndiponso njira zothandizira wodwala zimene mungalole mwa kuchita kulemba? Mutu 7 wa buku la “Chikondi cha Mulungu,” malifalensi amene atchulidwa ndiponso mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2006, zingakuthandizeni kusankha zinthu mwanzeru. Mukamawerenga malifalensi amene aikidwawo, onani ngati mungayankhe mafunso otsatirawa.

(1) Kodi chifukwa chachikulu chimene Mboni za Yehova zimakanira kuikidwa magazi n’chiyani? (2) Pa nkhani ya chithandizo cha mankhwala, kodi Mboni za Yehova zimafuna chiyani? (3) Kodi odwala ali ndi ufulu wotani? (4) N’chifukwa chiyani ndi nzeru ndiponso ndi udindo wa munthu aliyense kusankha chithandizo cha mankhwala chosagwiritsa ntchito magazi? (5) Ngati munthu wataya magazi ambiri, kodi madokotala ayenera kuchita zinthu ziwiri ziti mwamsanga? (6) Kodi mufunika kudziwa zinthu zotani zokhudza chithandizo cha mankhwala chosagwiritsa ntchito magazi? (7) Kodi n’zotheka kuchita maopaleshoni oopsa komanso ovuta popanda kuika munthu magazi? (8) Kodi pali kusintha kotani komwe kukuchitika m’zipatala zambiri?

Popeza kulandira thandizo lina lililonse limene latchulidwa m’malifalensiwa ndi nkhani ya chikumbumtima, musayembekezere kudzakumana kaye ndi vuto musanasankhe zimene mungavomere kapena kukana. Choncho ngati ndinu wobatizidwa, lemberanitu khadi lanu la DPA ndipo muziyenda nalo nthawi zonse.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

Kodi munasankha kale chithandizo chamankhwala ndiponso njira zothandizira wodwala zimene mungalole mwa kuchita kulemba?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena