Ndandanda ya Mlungu wa February 6
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 6
Nyimbo Na. 45 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 1 ndime 16-21 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yesaya 47-51 (Mph. 10)
Na. 1: Yesaya 51:1-11 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Mwambo wa Ukwati wa Adamu ndi Hava Unali Wotani?—rs tsa. 384 ndime 1-2 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Mulungu, Yemwe Ndi Wachikondi, Adzawononge Anthu Ena?—2 Ates. 1:6-9 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Malo Ochezera a pa Intaneti?—Gawo 2. Nkhani yochokera mu Galamukani! ya August 2011, masamba 10 mpaka 13 ndi Galamukani! ya February 2012, tsamba 8 ndi 9.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini M’mwezi wa Februaryy. Nkhani yokambirana. Kwa mphindi imodzi kapena ziwiri, fotokozani nkhani zochepa za m’magaziniwo zimene zingakhale zogwira mtima kwa anthu a m’gawo lanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti afotokoze mafunso okopa chidwi amene angagwiritse ntchito ndiponso malemba amene angawerenge. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira za mu Galamukani! Ndipo ngati nthawi ilipo fotokozaninso nkhani imodzi. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 96 ndi Pemphero