Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu January: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Muyesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo pa ulendo woyamba. February: Gawirani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March ndi April: Gawirani buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Komanso mugawire magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kwa anthu amene asonyeza chidwi, agawireni kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo.
◼ Kuyambira mwezi wa February, oyang’anira madera ayamba kukamba nkhani ya onse ya mutu wakuti, “Kodi Mumadalira Yehova?”
◼ Kuyambira ndi Nsanja ya Olonda yogawira ya February 1, 2012, muzikhala nkhani za mutu wakuti, “Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo.” Nkhanizi zakonzedwa kuti makolo aziphunzira ndi ana amene sanakwanitse zaka zitatu ndipo zizituluka mosinthanasinthana ndi nkhani za mutu wakuti, “Phunzitsani Ana Anu” ndi “Zoti Achinyamata Achite.”