Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/12 tsamba 4
  • Zitsanzo za Ulaliki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zitsanzo za Ulaliki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
km 1/12 tsamba 4

Zitsanzo za Ulaliki

Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa February

“Kodi mukuganiza kuti Mulungu ali ndi gulu linalake la anthu limene akulitsogolera, kapena amangochita zinthu ndi anthu pawokhapawokha? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene magazini iyi ikunena za anthu amene Mulungu anawasankha zaka zambiri zapitazo.” Tsegulani patsamba 16 la Nsanja ya Olonda ya February 1 ndipo muwerenge ndime imene ili pansi pa kamutu koyamba. Muwerengenso lemba limodzi mwa malemba amene ali pamenepo. Kenako gawirani magaziniyo ndipo mukonze zodzabweranso kuti mudzakambirane funso lotsatira.

Nsanja ya Olonda February 1

“Anthu akhala akukambirana kwambiri za Aramagedo zaka zaposachedwapa. Kodi mukuganiza kuti pali chilichonse chimene anthu angachite kuti Aramagedo isachitike? [Yembekezani ayankhe.] Mawu akuti Aramagedo amapezeka pa lemba ili. [Werengani Chivumbulutso 16:16. Kenako muonetseni magaziniwo.] Magazini iyi ili ndi mayankho a m’Baibulo a mafunso amenewa.”

Galamukani! February

Masiku ano, anthu ambiri amakonda kulankhulana pa Intaneti. Kodi mukuganiza kuti kulankhulana kwa mtundu umenewu kuli ndi vuto lililonse? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo lili ndi mfundo zimene zingatithandize kugwiritsa ntchito Intaneti mwanzeru. [Tsegulani patsamba 6 mpaka 9 ndipo mukambirane funso limodzi mwa mafunso amene ali pamenepo ndiponso lemba limene laikidwa pamenepo.] Magazini iyi ikuthandizani kudziwa ndiponso kupewa mavuto amene munthu angakumane nawo chifukwa chocheza ndi anthu ena pa Intaneti.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena