Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa September
“Anthu a m’mayiko osiyanasiyana komanso azipembedzo zosiyanasiyana amapemphera tsiku ndi tsiku. Kodi mukuganiza kuti Mulungu amamva komanso kuyankha mapemphero onse?” [Yembekezani ayankhe.] Kenako m’patseni Nsanja ya Olonda ya September 1 ndipo werengani ndi kukambirana naye nkhani imene ili pakamutu koyamba patsamba 16, komanso limodzi mwa malemba amene ali m’nkhaniyo. Ndiyeno mugawireni magaziniyi n’kukonza zoti mudzabwerenso kudzakambirana yankho la funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda September 1
Muonetseni chikuto cha magaziniwa ndipo funsani kuti: “Kodi inuyo mungayankhe bwanji funso limeneli?” [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena. [Werengani 1 Yohane 5:19.] Vesili likusonyeza kuti “woipayo,” kapena kuti Mdyerekezi ndi amene akulamulira dziko lapansili. Komabe, zimenezi zimachititsa ena kudzifunsa kuti: Kodi Satana anachokera kuti? Kodi Satana ndi munthu weniweni? Kodi Mulungu alola Satana kulamulira mpaka liti? Magazini iyi ikusonyeza zimene Baibulo limanena.”
Galamukani! September
Anthu ambiri masiku ano akuda nkhawa kwambiri chifukwa cha mavuto azachuma. Kodi mukuona kuti n’chifukwa chiyani masiku ano zikuvuta kupeza zosowa za tsiku ndi tsiku? [Yembekezani ayankhe.] M’Baibulo muli malangizo anzeru amene athandiza anthu ambiri kuti azigwiritsa ntchito ndalama mwanzeru. [Werengani limodzi mwa malemba amene ali patsamba 8 ndi 9.] Magazini iyi ili ndi mfundo zimene zingathandize kwambiri anthu amene akuvutika kubweza ngongole.”