Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa September
“Anthu ambiri amakhulupirira kuti tsiku lina Mulungu adzawaweruza mogwirizana ndi zochita zawo. Kodi mukuganiza kuti Tsiku la Chiweruzo tiyenera kuliyembekezera mwachidwi kapena kuliopa? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene magazini iyi ikunena.” M’patseni mwininyumba Nsanja ya Olonda ya September 1, ndipo kambiranani zimene zili pakamutu koyamba patsamba 16. Yesetsani kuwerenga ngakhale lemba limodzi. M’siyireni magaziniyo ndipo mukonze zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda September 1
“M’mayiko ambiri, akazi amasalidwa ndiponso amachitiridwa nkhanza. Ndipo n’zomvetsa chisoni kuti zikhulupiriro zina za chipembedzo n’zimene zimachititsa zimenezi. Kodi Mulungu amaona kuti akazi ndi otsika? [Yembekezani ayankhe.] Taonani malangizo a m’Baibulo onena za mmene amuna ayenera kuchitira zinthu ndi akazi awo. [Werengani Aefeso 5:28, 29.] Magaziniyi ikusonyeza zimene Baibulo limanena zokhudza mmene Mulungu amaonera akazi.”
Galamukani! September
“Anthu ambiri amanena kuti tsiku lina zinthu zonse zamoyo zidzafa padzikoli chifukwa cha nkhondo ya zida zoopsa kapena tsoka lachilengedwe. Iwo amati chimwala chidzagwa kuchokera kumwamba n’kuphwanyiratu dzikoli, kapenanso zinthu zonse zidzafa chifukwa cha kusintha kwa nyengo. Kodi mukuganiza kuti zinthu ngati zimenezi zidzachitikadi kapena anthu amangonena za m’maganizo mwawo? [Yembekezani ayankhe.] Tiyeni tione mfundo yolimbikitsa imene Baibulo limalonjeza. [Werengani Salimo 37:29.] Magaziniyi ikufotokoza zimene anthu ambiri amaganiza pa nkhani ya kutha kwa dzikoli, komanso mfundo za m’Baibulo zolimbikitsa zokhudza zimene zidzachitike m’tsogolo.”