Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa September
“Anthu ambiri amakhulupirira angelo. Kodi nanunso mumawakhulupirira? [Yembekezerani ayankhe.] Angelo ndi zolengedwa zauzimu ndipo ndi amphamvu kwambiri. Kodi inuyo mumaona kuti angatithandize? Baibulo limanena mmene angelo amathandizira anthu masiku ano.” Asonyezeni funso loyamba limene lili patsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya September 1. Kambiranani ndime zimene zili pansi pa funso loyamba komanso lemba limodzi pa malemba amene ali kumapeto kwa ndimezo. Agawireni magaziniyo, ndipo konzani zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda September 1
“Kodi mukuona kuti anthu awononga dzikoli mpaka kufika poti silingakonzedwenso? [Yembekezerani ayankhe.] Anthu sangathe kubwezeretsa zinthu zachilengedwe zimene zawonongedwa padzikoli. Koma Baibulo limatiuza kuti Mulungu adzakonza zinthu padzikoli ndipo ndi wofunitsitsa kuchita zimenezi. Lemba la Salimo 65:9 limatitsimikizira zimenezi. [Werengani.] Magaziniyi ikufotokoza zimene Mulungu adzachite kuti akonze dzikoli komanso zimene ifeyo tingachite kuti tidzasangalale ndi madalitso amene watikonzera m’tsogolo. Kodi mungakonde ndikupatseni kuti muwerenge?”
Galamukani! September
“Anthu ambiri amaona kuti mabwana awo amafuna kuti azigwira ntchito maola ochuluka. Anthuwa amaona kuti palibe chimene angachite kuti zimenezi zisamachitike. Akatswiri amanena kuti ngati munthu akugwira ntchito maola ambiri, zingapangitse kuti ayambe kupanikizika ndi ntchito. Izi zingayambitse mavuto osiyanasiyana monga matenda a maganizo. Kodi mukuganiza kuti munthu angatani kuti asamapanikizike ndi ntchito? [Yembekezerani ayankhe.] Tiyeni tiwerenge lemba lochititsa chidwi ili. [Werengani Mlaliki 4:6.] Magaziniyi ikufotokoza zinthu 4 zimene tingachite kuti tisamapanikizike ndi ntchito.”