Zochitika mu Utumiki Wakumunda
M’mwezi wa March, womwe unali chiyambi cha nyengo yachikumbutso, tinagawira magazini okwana 445,963. Komanso tinachititsa maphunziro a Baibulo okwana 91,803. Tikukuthokozani kwambiri abale ndi alongo nonse chifukwa cha khama lanu pofunafuna anthu oyenera uthenga wabwino.—Mat. 10:11.