Ndandanda ya Mlungu wa September 12
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 12
Nyimbo Na. 22 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 12 ndime 15-21 ndi bokosi patsamba 127 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 120-134 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 124:1–126:6 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Ufumu wa Mulungu Udzabweretsa Chikondi ndi Mgwirizano Padziko Lonse—rs tsa. 380 ndime 3 mpaka 5 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingakhale Bwanji Ndi “Diso Lolunjika pa Chinthu Chimodzi”?—Mat. 6:22, 23 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo. Kambiranani “Zochitika mu Utumiki Wakumunda” zimene zili patsamba 4. Yamikirani mpingo chifukwa chothandiza nawo kuti lipoti la mwezi wa April likhale labwino kwambiri.
Mph. 10: Mmene Tingawafikire Pamtima—Gawo 1. Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 258 mpaka tsamba 260, ndime 5. Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza wofalitsa akugwiritsa ntchito mfundo imodzi kapena ziwiri zochokera mu nkhaniyi.
Mph. 10: Sukudziwa Pamene Padzachite Bwino. (Mlal. 11:6) Nkhani yokambirana yochokera mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2008, tsamba 12 ndime 1 mpaka 3, ndiponso tsamba 17, ndime 1 ndi 2. Pemphani omvera kuti anene zimene aphunzirapo.
Mph. 10: “Muziona Mwayi Wanu wa Utumiki Monga Chinthu Chamtengo Wapatali.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 34 ndi Pemphero