Zilengezo
◼ Mabuku ogawira m’mwezi wa August: Gawirani kabuku kalikonse kamasamba 32 kamene anthu angachite nako chidwi m’gawo lanu monga: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dikirani!, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Sangalalani Ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! ndi kakuti, “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” September: Gawirani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo pa ulendo woyamba. October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati mwininyumba wasonyeza chidwi, m’gawireni kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo. November: Gawirani kabuku kakuti Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani? Kapena mungagawire kabuku kalikonse pa timabuku tamasamba 32 timene tatchulidwa kumayambiriroku, togawira mu August 2011.