Ndandanda ya Mlungu wa September 5
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 5
Nyimbo Na. 2 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 12 ndime 8-14 (Mph. 25)
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
Kuwerenga Baibulo: Salimo 119 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 119:49-72 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Malemba Amatilimbikitsa Kuti Tiziopa Yehova?—Deut. 5:29 (Mph. 5)
Na. 3: Ufumu wa Mulungu Udzaukitsa Akufa—rs tsa. 379 ndime 6 –tsa. 380 ndime 2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Machitidwe 5:17-42. Kenako, kambiranani mmene nkhani imeneyi ingatithandizire pa utumiki wathu.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Konzekerani Utumiki ndi Banja Lanu. Kufunsa komanso chitsanzo. Funsani mabanja awiri, banja lina likhale la mwamuna ndi mkazi yekha ndipo linalo likhale loti lili ndi ana. Mabanjawa afotokoze mmene amakonzekerera utumiki wakumunda pa nthawi ya Kulambira kwa Pabanja. Kenako mutu wabanja mmodzi ndi banja lake achite chitsanzo chosonyeza mmene angachitire pokonzekera utumiki wa Loweruka.
Nyimbo Na. 41 ndi Pemphero