Zochitika mu Utumiki Wakumunda
M’chaka chapitachi cha 2011, m’Malawi muno munachitika misonkhano yachigawo yokwana 69 ndipo anthu 243,470 anapezeka pa misonkhano imeneyi. Komanso pa misonkhano imeneyi anthu okwana 2,588 anasonyeza kudzipereka kwawo kwa Yehova mwa kubatizidwa. Zimenezi zikusonyeza kuti pali anthu ambiri amene akufunikira thandizo lathu kuti apite patsogolo mwauzimu.—Mat. 28:19-20.