Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/11 tsamba 2
  • Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Kodi Chithandizo Chamankhwala Chabwino Kwambiri N’chiti?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Kodi Mumanyalanyaza?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Kodi Mumanyalanyaza?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
km 1/11 tsamba 2

Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?

Masiku ano m’zipatala zambiri padziko lonse, odwala amawapanga opaleshoni popanda kuwaika magazi. Kodi mukudziwa bwino zithandizo za mankhwala zosagwiritsa ntchito magazi zimene mungathe kusankha? Muyenera kudziwa zimenezi kuti muzitha kusankha bwino chithandizo cha mankhwala kapena mtundu wa opaleshoni. Kuti muphunzire zambiri zokhudza nkhani imeneyi, werengani mofatsa mutu 7 m’buku lakuti Khalanibe M’chikondi cha Mulungu ndiponso malifalensi amene asonyezedwa m’nkhaniyi. Pambuyo pake, pempherani ndipo pogwiritsa ntchito mafunso amene ali m’munsimu, ganizirani zimene mwaphunzirapo.

(1) Kodi chifukwa chachikulu chimene Mboni za Yehova zimakanira kuikidwa magazi n’chiyani? (2) Pa nkhani ya chithandizo cha mankhwala, kodi Mboni za Yehova zimafuna chiyani? (3) Kodi odwala ali ndi ufulu wotani? (4) N’chifukwa chiyani ndi nzeru ndiponso ndi udindo wa munthu aliyense kusankha chithandizo cha mankhwala chosagwiritsa ntchito magazi? (5) Ngati munthu wataya magazi ambiri, kodi madokotala ayenera kuchita zinthu ziwiri ziti mwamsanga? (6) Kodi mufunika kudziwa zinthu zotani zokhudza chithandizo cha mankhwala chosagwiritsa ntchito magazi? (7) Kodi n’zotheka kuchita maopaleshoni oopsa komanso ovuta popanda kuika munthu magazi? (8) Kodi pali kusintha kotani komwe kukuchitika m’zipatala zambiri?

Zithandizo zina zimene zasonyezedwa m’bukuli n’zoti munthu aliyense asankhe payekha mogwirizana ndi chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo. Kodi mwasankha kale chithandizo chamankhwala chimene mungathe kulandira ndiponso chimene mungalole kuti ana anu apatsidwe komanso kulemba zomwe mwasankhazo pa Khadi Lopatsa Munthu Mphamvu Yosasinthika Yondisankhira Thandizo la Mankhwala (DPA)? Kuti mumve zambiri pa nkhani imeneyi, werengani mofatsa “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” a mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2004, ndiponso ya October 15, 2000. Kenako gwiritsani ntchito zikalata zimene zili mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2006, yamutu wakuti “Kodi Ndimaiona Bwanji Nkhani Yokhudza Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zachipatala Zogwiritsa Ntchito Magazi Anga Omwe?,” posankha zimene mukuvomereza kapena kukana. Pomaliza, onetsetsani kuti mwalemba bwinobwino zimene mwasankhazo pakhadi lanu la DPA. Anthu omwe mwawasankha kukuimirani ndiponso achibale anu omwe si Mboni ayenera kudziwa bwino zosankha zanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena