Ndandanda ya Mlungu wa January 24
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 24
Nyimbo Na. 53 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 1 ndime 16-20, ndi bokosi la patsamba 13 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ezara 6-10 (Mph. 10)
Na. 1: Ezara 7:1-17 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Mmene Yesu Anasonyezera Kuti Ndi Woyenera Kukhala Mfumu (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Yesu Khristu ndiye Mulungu?—rs tsa. 426 ndime 1 ndi 2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo. Tchulani mabuku ogawira mwezi wa February, ndipo chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagawire limodzi mwa mabukuwo.
Mph. 20: “Mphatso Yothandiza kwa Mabanja.”—Gawo 1. (Ndime 1-6 ndi bokosi la patsamba 6.) Mafunso ndi mayankho. Limbikitsani omvera kuti akayeserere zina mwa mfundo zimene zili m’bokosi patsamba 6 akamakachita Kulambira kwa Pabanja. Mlungu wotsatira, mukamadzakambirana mbali yomalizirayi, iwo adzakhala ndi mwayi wofotokoza mmene banja lawo lapindulira.
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Magazini M’mwezi wa February. Nkhani yokambirana. Fotokozani zimene zili m’magaziniwo kwa mphindi imodzi kapena ziwiri. Kenako sankhani mitu iwiri kapena itatu, ndipo funsani omvera kuti afotokoze mafunso ndiponso malemba amene angagwiritse ntchito pogawira magaziniwo. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawire magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 32 ndi Pemphero