Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/09 tsamba 3
  • Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Kodi Mumanyalanyaza?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Kodi Chithandizo Chamankhwala Chabwino Kwambiri N’chiti?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Kodi Mumanyalanyaza?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 1/09 tsamba 3

Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?

Masiku ano m’zipatala zambiri padziko lonse, odwala amawapanga opaleshoni popanda kuwaika magazi. Kodi mukudziwa bwino zithandizo za mankhwala zosaphatikizapo kuika munthu magazi zimene mungasankhe? Muyenera kudziwa zimenezi kuti muthe kusankha bwino chithandizo cha mankhwala kapena mtundu wa opaleshoni. Kuti mumve zambiri pankhani imeneyi, werengani bwinobwino “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2004 ndi ya October 15, 2000. Pambuyo pake, pempherani ndi kuganizira zimene mwaphunzira kuti muone zimene mungasankhe pogwiritsa ntchito mafunso otsatirawa.

(1) Kodi chifukwa chachikulu chimene Mboni za Yehova zimakanira kuikidwa magazi n’chiyani? (2) Pa za chithandizo cha mankhwala, kodi Mboni za Yehova zimafuna chiyani? (3) Kodi odwala ali ndi ufulu wotani? (4) N’chifukwa chiyani ndi nzeru ndiponso ndi udindo wa munthu aliyense kusankha zithandizo za mankhwala zosaphatikizapo kuikidwa magazi? (5) Kodi mufunika kudziwa zinthu zotani zokhudza chithandizo cha mankhwala chosaphatikizapo kuika magazi? (6) Kodi n’zotheka kuchita maopaleshoni oopsa komanso ovuta popanda kuika magazi?

Zithandizo zina zimene zasonyezedwa mu zofalitsa zili m’nkhani ino n’zoti munthu aliyense asankhe payekha mogwirizana ndi chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo. Kodi mwasankha zithandizo za mankhwala zimene inuyo ndi ana anu mungavomere kulandira? Ndipo kodi mwazilemba pa khadi la DPA? Gwiritsani ntchito zikalata zimene zili mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2006, yamutu wakuti “Kodi Ndimaiona Bwanji Nkhani Yokhudza Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zachipatala Zogwiritsa Ntchito Magazi Anga Omwe?,” posankha zimene mukuvomereza kapena kukana. Pomaliza, onetsetsani kuti mwalemba bwinobwino zimene mwasankhazo pakhadi lanu la DPA. Anthu omwe mwawasankha kukuimirani ndiponso achibale anu omwe si Mboni ayenera kudziwa bwino zosankha zanu.

[Bokosi patsamba 3]

• Kodi mwasankha zithandizo za mankhwala zimene inuyo ndi ana anu mungavomere kulandira?

• Kodi mumayenda ndi khadi la DPA lolembedwa bwino kuti likuthandizeni pa zinthu zogwa mwadzidzidzi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena