Ndandanda ya Mlungu wa February 2
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 2
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 13, ndime 19-23 ndi bokosi
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Genesis 21-24
Na. 1: Genesis 22:1-18
Na. 2: “Uyu Ndiye Mwana Wanga” (lr-CN mutu 5)
Na. 3: Njira Zimene Tingafutukulire Chikondi Chathu pa Ena (2 Akor. 6:11-13)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa January.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Zimene Anthu Amanena Zomwe Zingalepheretse Kukambirana Nawo. Lankhulani mawu oyamba mwachidule, ndipo kenako pogwiritsa ntchito buku la Kukambitsirana, tsamba 15-20, khalani ndi chitsanzo chosonyeza mmene tingayankhire anthu m’gawo lathu ngati anena mawu osonyeza kuti sakufuna kuti tikambirane nawo.
Mph. 10: Thandizani Amene Sakhulupirira Baibulo. Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Kukambitsirana, tsamba 58-62. Kambiranani zimene tinganene pa mfundo zosiyanasiyana zimene anthu amanena zotsutsa Baibulo. Khalani ndi chitsanzo chosonyeza mmene tingayankhire mawu amene anthu amakonda kunena m’gawo lathu.