Ndandanda ya Mlungu wa January 26
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 26
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 13, ndime 9-18
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Genesis 17-20
Na. 1: Genesis 17:1-17
Na. 2: Chifukwa Chake Anthu Alephera Kukhazikitsa Boma Lachilungamo (rs-CN tsa. 62 mpaka tsa. 63 ndime 4)
Na. 3: Mulungu Ali ndi Dzina Lake (lr-CN mutu 4)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Magazini ya Nsanja ya Olonda ya February 1 ndi Galamukani! ya February. Kukambirana ndi omvera. Fotokozani mwachidule mfundo za m’magaziniwa ndipo funsani omvera kuti atchule nkhani zimene zingachititse chidwi anthu a m’gawo lanu ndipo anene chifukwa chake. Pemphani omvera kuti atchule zimene anganene poyamba kukambirana ndi munthu. Kodi ndi mafunso komanso malemba ati amene angagwiritse ntchito asanagawire magazini? Malizani nkhaniyi ndi chitsanzo cha mmene tingagawire magazini iliyonse pogwiritsa ntchito mfundo za patsamba 4 kapena mfundo zimene omvera anena.
Mph. 20: “Kodi Mukudziwa Zimene Mungasankhe?”a Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Pomaliza, werengani ndime yothera.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu anu oyamba asafike mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.