Ndandanda ya Mlungu wa January 30
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 30
Nyimbo Na. 47 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 1 ndime 10-15 ndi tchati patsamba 12 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yesaya 43-46 (Mph. 10)
Na. 1: Yesaya 45:15-25 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Kuleza Mtima Kwa Mulungu Kungatithandize Bwanji Kuti Tidzapulumuke?—2 Pet. 3:9, 15 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi N’zofunikadi Kutsatira Malamulo a Boma Okhudza Kumangitsa Ukwati?—rs tsa. 383 ndime 1-3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 4, chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungayambitsire phunziro pa Loweruka loyambirira m’mwezi wa February.
Mph. 10: Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Malo Ochezera a pa Intaneti?—Gawo 1. Nkhani yochokera mu Galamukani! ya July 2011, masamba 24 mpaka 27 ndi Galamukani! ya February 2012, tsamba 6 ndi 7.
Mph. 20: “Kodi Mwakonzekera Ngati Mutachita Ngozi?” Mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mfundo za m’ndime yoyamba ndi yomaliza monga mawu oyamba ndi omaliza.
Nyimbo Na. 116 ndi Pemphero