Ndandanda ya Mlungu wa January 23
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 23
Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 1 ndime 1-9 ndi kalata patsamba 2 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yesaya 38-42 (Mph. 10)
Na. 1: Yesaya 39:1-8 ndi Yesaya 40:1-5 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Madalitso Amene Tikuyembekezera Adzakwaniritsidwa Bwanji?—rs tsa. 293 ndime 1-3 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Maphunziro Omwe Mulungu Amatipatsa Amaposa Bwanji Maphunziro Adziko?—Afil. 3:8 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Tchulani mabuku ogawira m’mwezi wa February ndipo chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri zosonyeza mmene tingagawirire mabukuwa.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Maliko 10:17-30. Kambiranani mmene mavesi amenewa angatithandizire mu utumiki.
Mph. 15: Khalani Ndi Khalidwe Labwino Pakati pa Anthu a M’dzikoli. (1 Pet. 2:12) Nkhani yokambirana yochokera mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2009, tsamba 19, ndime 13-15. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene aphunzirapo.
Nyimbo Na. 112 ndi Pemphero