Ndandanda ya Mlungu wa January 25
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 25
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv mutu 2, ndime 12-21 ndi bokosi patsamba 24a
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Oweruza 5-7
Na. 1: Oweruza 7:1-11
Na. 2: Kodi Tingamudziwe Bwanji “Mkazi Wachiwerewere Wamkulu” Wotchulidwa pa Chivumbulutso 17:1?
Na. 3: Kodi Pali Munthu Aliyense Amene Anayamba Watuluka mu Helo Wotchulidwa M’Baibulo? (rs tsa. 145 ndime 5.)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Mabuku Ogawira mu February. Fotokozani mwachidule mfundo zikuluzikulu za m’buku limene tidzagawire mu February. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akuchita ulaliki wamwamwayi n’kugawira bukulo ndiponso kuyambitsa phunziro la Baibulo.
Mph. 20: “Kodi Mumanyalanyaza?” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mkulu. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akufotokozera dokotala ntchito ya khadi la DPA ndi kumupempha kuti alisunge m’faelo ya wofalitsayo. Dokotalayo akulonjeza kuti adzatero. Pomaliza, werengani ndime yomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Mungasankhe kukambirana bokosi kapena ayi.