Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 October tsamba 8
  • Kodi Mukugwiritsa Ntchito Bwino Makadi Odziwitsa Anthu za JW.ORG?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukugwiritsa Ntchito Bwino Makadi Odziwitsa Anthu za JW.ORG?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Makhadi a Ngongole Kodi Adzakutumikirani Kapena Kukupangani Kapolo?
    Galamukani!—1997
  • Kodi Ndikhale ndi Khadi la Ngongole?
    Galamukani!—2000
  • Muzigwiritsa Ntchito Tsamba Loyamba la JW.ORG Mukakhala mu Utumiki
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Zinthu Zotithandiza Kuti Tipeŵe Magazi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 October tsamba 8

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mukugwiritsa Ntchito Bwino Makadi Odziwitsa Anthu za JW.ORG?

Wa Mboni za Yehova akupatsa munthu khadi lodziwitsa anthu za jw.org

Popeza kuti chisautso chachikulu chayandikira, tiyenera kugwira ntchito yolalikira mwakhama kwambiri. (Miy. 24:11, 12, 20) Tikhoza kuthandiza anthu kuphunzira Baibulo komanso kupita pawebusaiti yathu pogwiritsa ntchito makadi odziwitsa anthu za jw.org. Makadiwa amakhala ndi kachidindo kothandiza anthu kuti apite pawebusaitiyi n’kupempha kuti aziphunzira Baibulo. Kachidindoka kamawathandizanso kuti aonere vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? Anthu ena safuna kulandira mabuku athu koma angafune kupita pawebusaiti yathu. Choncho ndi bwino kuwapatsa makadiwa. Komabe si bwino kupatsa makadiwa anthu amene alibe chidwi.

Mukhoza kugawira makadiwa kwa anthu amene mumakumana nawo tsiku ndi tsiku. Mungayambe ndi kunena kuti: “Ndili ndi khadi limene ndikufuna ndikupatseni. Khadili lingakuthandizeni kupita pawebusaiti yaulere yomwe ili ndi nkhani komanso mavidiyo osiyanasiyana.” (Yoh. 4:7) Popeza kuti makadiwa ndi aang’ono, simungavutike kuwanyamula kulikonse kumene mungapite n’kumagawira anthu omwe mwakumana nawo.

MUZIPEREKA MAKADIWA KWA ANTHU . . .

  • mukamalalikira mwamwayi

  • mukamalalikira m’maofesi ndi m’mashopu

  • ngati amvetsera uthenga wathu koma sakufuna kulandira mabuku

Chithunzi cha Baibulo lotsegula chomwe chili pakhadi lodziwitsa anthu za jw.org
A jw.org contact card showing one of Jehovah’s Witnessing reading a scripture to a person
Chithunzi cha wa Mboni za Yehova akuwerengera munthu lemba chomwe chili pakhadi lodziwitsa anthu za jw.org
Mmene khadi lodziwitsa anthu za jw.org limaonekera kuseri kwake

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena