Ndandanda ya Mlungu wa March 16
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 16
Nyimbo Na. 1 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 10 ndime 1-7 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Samueli 5-9 (Mph. 8)
Na. 1: 1 Samueli 6:10-21 (Osapitirira mph. 3)
Na. 2: Musakhale Ngati Yezebeli—Chiv. 2:18-23 (Mph. 5)
Na. 3: Akhristu Enieni Amakondana—bt tsa. 74-76 ndime 22-24 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: ‘Khalani Okonzekera Ntchito Iliyonse Yabwino.’—Tito 3:1.
Mph. 10: Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Taiwan. Nkhani yokambirana yochokera mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2014, tsamba 3 mpaka 6. Kodi ofalitsa omwe atchulidwa m’nkhaniyi anakonzekera bwanji kusamukira kudziko lina? Nanga apeza madalitso otani?
Mph. 20: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Pezani Anthu Oti Muziwapatsa Magazini Mwezi Uliwonse.” Nkhani yokambirana. Mukamaliza kukambirana nkhaniyi, chitani chitsanzo chachidule chosonyeza wofalitsa akuuza munthu yemwe amam’patsa magazini kuti angathe kumaphunzira naye Baibulo. Kenako funsani wofalitsa amene ali ndi anthu amene amawapatsa magazini nthawi zonse. Kodi anthuwo alipo angati? Nanga amakonzekera bwanji akamapita kwa anthuwo? Afotokozenso zosangalatsa zomwe anakumana nazo.
Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero