Ndandanda ya Mlungu wa January 27
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 27
Nyimbo Na. 120 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 6 ndime 19-24 ndi bokosi patsamba 78 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Genesis 17-20 (Mph. 10)
Na. 1: Genesis 17:18-27 mpaka 18:1-8 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Yesu Sanapite Kumwamba Ndi Thupi Lanyama—rs tsa. 107 ndime 2–tsa. 108 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Babulo Wamkulu N’chiyani?—bh tsa. 219-220 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Yambitsani Phunziro la Baibulo Loweruka Loyambirira. Nkhani. Tchulani zimene mpingo wanu wakonza podzayambitsa maphunziro Loweruka loyambirira la mwezi wa February ndipo limbikitsani ofalitsa onse kuti adzayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Chitani chitsanzo cha mmene tingayambitsire maphunziro pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chomwe chili patsamba 4.
Mph. 15: Kodi Muli ndi Zolinga Zotani Zauzimu? Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Gulu, patsamba 117 ndime 1 mpaka kumapeto kwa mutuwo. Funsani wofalitsa mmodzi kapena awiri amene anakwaniritsa cholinga chawo chochita utumiki wa nthawi zonse. Kodi anthu ena anawalimbikitsa bwanji? Kodi anakumana ndi mavuto otani? Nanga apeza madalitso ati?
Mph. 10: “Tingathe Kuyambitsa Phunziro kwa Anthu Amene Timawapatsa Magazini.” Mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene anayambitsira phunziro kwa munthu amene ankamupatsa magazini.
Nyimbo Na. 103 ndi Pemphero