-
Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo ndi Ndani?Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
-
-
Mkulu wa Angelo. Mawu a Mulungu amanena kuti Mikayeli ndi “mkulu wa angelo.” (Yuda 9) Mmene dzina lakuti “mkulu wa angelo” limalembedwera zimasonyeza kuti akunena za munthu mmodzi. Zimenezi zikusonyeza pali mngelo mmodzi yekha amene ali ndi udindo umenewu. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti udindo umenewu ndi wa Yesu. Pofotokoza za Yesu Khristu ataukitsidwa, lemba la 1 Atesalonika 4:16 limanena kuti: “Ambuye . . . adzatsika kumwamba, ndi mfuu yolamula ya mawu a mkulu wa angelo.” Pa lemba limeneli, mawu a Yesu akufotokozedwa kuti ndi mawu a mkulu wa angelo. Choncho, Baibulo limasonyeza kuti Mikayeli mkulu wa angelo ndi Yesu.
Mtsogoleri wa Gulu Lankhondo. Baibulo limanena kuti “Mikayeli ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. . . . ndi angelo ake.” (Chivumbulutso 12:7) Choncho, Mikayeli ndi Mtsogoleri wa gulu lankhondo la angelo okhulupirika. Buku la Chivumbulutso limatchulanso kuti Yesu ndi Mtsogoleri wa gulu lankhondo la angelo okhulupirika. (Chivumbulutso 19:14-16) Ndipo mtumwi Paulo anatchula za “Ambuye Yesu” ndi “angelo ake amphamvu.” (2 Atesalonika 1:7) Choncho Baibulo limanena za Mikayeli ndi “angelo ake,” ndiponso Yesu ndi “angelo ake.” (Mateyu 13:41; 16:27; 24:31; 1 Petulo 3:22) Popeza Baibulo silisonyeza zoti pali magulu awiri a angelo okhulupirika, lina lotsogoleredwa ndi Mikayeli ndipo lina lotsogoleredwa ndi Yesu, n’zomveka kunena kuti Mikayeli ndi dzina la Yesu Khristu pa udindo umene ali nawo kumwamba.a
-
-
Kodi “Babulo Wamkulu” N’chiyani?Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
-
-
ZAKUMAPETO
Kodi “Babulo Wamkulu” N’chiyani?
M’BUKU la Chivumbulutso muli mawu ambiri okuluwika. (Chivumbulutso 1:1) Mwachitsanzo, limafotokoza za mkazi wina yemwe analembedwa dzina lakuti “Babulo Wamkulu” pamphumi pake. Mkaziyu amamufotokoza kuti wakhala pa ‘makamu a anthu ndi mayiko.’ (Chivumbulutso 17:1, 5, 15) Popeza palibe mkazi aliyense amene angathe kuchita zimenezi, ndiye kuti mawu akuti Babulo Wamkulu ndi okuluwika. Ndiye kodi hule limeneli likuimira chiyani?
Pa Chivumbulutso 17:18, mkazi yemweyu akufotokozedwa kuti ndi “mzinda waukulu umene ukulamulira mafumu a dziko lapansi.” Mawu akuti “mzinda” akusonyeza kuti limeneli ndi gulu la anthu omwe amachita zinthu mogwirizana. Popeza “mzinda waukulu” umenewu umalamulira “mafumu a dziko lapansi,” ndiye kuti mkazi amene amatchulidwa kuti Babulo Wamkulu ayenera kukhala gulu lomwe zochita zake zimakhudza dziko lonse lapansi, moti n’zomveka kunena kuti ndi ufumu wa padziko lonse. Ufumu umenewu, kapena kuti ulamuliro, ndi wachipembedzo. Tiyeni tione nkhani zina za m’buku la Chivumbulutso zimene zikutichititsa kuona choncho.
Ulamuliro ukhoza kukhala m’manja mwa anthu andale, abizinezi, kapena achipembedzo. Mkazi yemwe akutchulidwa kuti ndi Babulo Wamkuluyu sakuimira ulamuliro wa andale, chifukwa mawu a Mulungu amanena kuti ‘mafumu a dziko lapansi anachita naye dama.’ Dama lake ndi lakuti wakhala akugwirizana ndi olamulira adziko lapansi ndiponso kuchita zinthu zina zambiri n’cholinga choti aziwalamulira. N’chifukwa chake amatchulidwa kuti ndi “hule lalikulu.”—Chivumbulutso 17:1, 2; Yakobo 4:4.
Babulo Wamkulu sangakhalenso ulamuliro wa anthu abizinezi chifukwa “amalonda oyendayenda a padziko lapansi,” kutanthauza anthu abizinezi, adzamulira akadzawonongedwa. Ndipotu Baibulo limanena kuti mafumu ndi amalonda oyendayenda azidzayang’ana Babulo Wamkulu ataima “patali.” (Chivumbulutso 18:3, 9, 10, 15-17) Choncho, n’zomveka kunena kuti Babulo Wamkulu si ulamuliro wa andale kapena abizinezi, koma wachipembedzo.
Umboni wina wosonyeza kuti Babulo Wamkulu ndi ulamuliro wachipembedzo ndi wakuti amanenedwa kuti amasocheretsa mitundu yonse ya anthu ndi ‘zochita zake zamizimu.’ (Chivumbulutso 18:23) Popeza zinthu zonse zamizimu zimachokera kwa ziwanda, n’chifukwa chake Baibulo limanena kuti Babulo Wamkulu ndi “malo okhala ziwanda.” (Chivumbulutso 18:2; Deuteronomo 18:10-12) Baibulo limafotokozanso kuti ulamuliro umenewu umalimbana ndi chipembedzo choona, moti umazunza “aneneri” ndiponso anthu “oyera.” (Chivumbulutso 18:24) Ndipotu Babulo Wamkulu amadana kwambiri ndi chipembedzo choona mpaka kufika pozunza mwankhanza komanso kupha “mboni za Yesu.” (Chivumbulutso 17:6) Zinthu zonsezi zikusonyeza kuti Babulo Wamkulu ndi zipembedzo zonse zonyenga zimene zimatsutsana ndi Yehova Mulungu.
-