Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kugawira Buku Lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’kofunika? Buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndi limene timaligwiritsa ntchito kwambiri pophunzitsa anthu Baibulo. Koma tisanayambe kuphunzira ndi munthu timafunika kumugawira bukuli. Choncho tiyenera kuyesetsa kugawira bukuli mwaluso. (Miy. 22:29) Pali njira zambiri zimene tingagwiritse ntchito pogawira bukuli koma aliyense angagwiritse ntchito njira imene akuona kuti imamuthandiza.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Pa Kulambira kwa Pabanja muziyesera njira zimene takambiranazi.
Mukakhala mu utumiki muziuza anzanu njira imene mukufuna kugwiritsa ntchito. (Miy. 27:17) Muzisintha ngati njirayo sikuthandiza.