Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tizisonyeza Anthu Mmene Timaphunzirira Baibulo Pogwiritsa Ntchito Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’kofunika? Tikauza anthu kuti timaphunzira Baibulo ndi anthu kwaulere, ambiri sadziwa kuti phunziroli limachitika bwanji. Ena amaganiza kuti ndiye kuti alowa kagulu kenakake kophunzira Baibulo kapena tiwapatsa zinazake zoti aziphunzira kunyumba, n’kumawayendera kuti tiziona mmene akuchitira. Choncho m’malo mongowauza kuti tingathe kumaphunzira nawo, ndi bwino kuwasonyeza mmene timachitira phunziro la Baibulolo. Tingathe kuchita zimenezi kwa mphindi zochepa, ngakhale tili chiimire. Zimenezi zingathandize munthu kuona kuti phunziro la Baibulo ndi lothandiza komanso losavuta.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni kuyambitsa phunziro la Baibulo.—Afil. 2:13.
Nthawi zonse mukamalalikira, yesetsani kusonyeza munthu mmene timaphunzirira Baibulo pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Mungathenso kumuonetsa vidiyo yakuti, Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji?