Ndandanda ya Mlungu wa December 15
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 15
Nyimbo Na. 114 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 5 ndime 18-21 ndi bokosi patsamba 55 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yoswa 6-8 (Mph. 10)
Na. 1: Yoswa 8:18-29 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chiyani Chimatsimikizira Kuti Munthu Ali Ndi Mzimu Woyera?—rs tsa. 320 ndime 3–tsa. 321 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Satana Mdyerekezi Ndi Mdani Wathu Wamkulu?—rs tsa. 352 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: Tizipereka zinthu “zabwino” zochokera m’chuma chomwe tinapatsidwa.—Mat. 12:35a.
Mph. 15: “Tizichititsa Maphunziro a Baibulo Mogwira Mtima.” Mafunso ndi mayankho. Mukamaliza kukambirana ndime 3, chitani chitsanzo cha mbali ziwiri chosonyeza wofalitsa ndi wophunzira Baibulo akukambirana ndime 8, mutu 15 m’buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Chitsanzo choyamba chisonyeze wofalitsayo akulankhula zinthu zambirimbiri. Pomwe chachiwiri chisonyeze wofalitsayo akufunsa wophunzirayo mafunso n’cholinga choti adziwe zomwe akuganiza.
Mph. 15: Zinthu Zimene Tingagwiritse Ntchito Pokonzekera Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo. Nkhani yokambirana. Kumbutsani abale za timapepala 6 tomwe tinatuluka pa msonkhano wachigawo wa 2013 komanso kamene katuluka pa msonkhano wachigawo wa chaka chino. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akulankhula yekha. Wofalitsayo akuganizira mavuto omwe anthu a m’dera lake amakumana nawo ndipo akukonzekera mafunso amene angagwiritse ntchito poyamba kukambirana ndi anthu. Pomaliza limbikitsani onse kuti aziphunzitsa mwaluso n’cholinga choti azifika anthu pamtima pogwiritsa ntchito zinthu zabwino zomwe tili nazo.—Miy. 20:5.
Nyimbo Na. 99 ndi Pemphero