Tizichititsa Maphunziro a Baibulo Mogwira Mtima
1. Kodi ofalitsa amene amachititsa maphunziro ali ndi udindo wotani?
1 Kuti munthu ayambe kutumikira Yehova amachita “kukokedwa” ndi iye. (Yoh. 6:44) Ngakhale zili choncho, ofalitsa ayenera kuyesetsa kuti athandize munthu amene akuphunzira nayeyo kuti akhale pa ubwenzi ndi Atate wathu wakumwamba. (Yak. 4:8) Koma kuchita zimenezi kumafuna kukonzekera. Kungowerenga ndime, n’kufunsa funso sikungathandize kwenikweni munthuyo kumvetsa uthenga wa m’Baibulo. Sikungamuthandizenso kuti azitsatira zimene waphunzirazo pa moyo wake.
2. Kodi tiyenera kuthandiza munthu amene tikuphunzira naye Baibulo kuchita zinthu zitatu ziti?
2 Pophunzira ndi munthu Baibulo, wofalitsa ayenera kuthandiza wophunzirayo kumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa, kuvomereza kuti n’zolondola ndiponso kuzitsatira pa moyo wake. (Yoh. 3:16; 17:3; Yak. 2:26) Komatu kuti munthu ayambe kuchita zimene Yehova amafuna komanso kuti adzipereke kwa iye, zimatenga nthawi yaitali. Choncho pamafunika kuleza mtima.
3. Kodi tingadziwe bwanji zimene wophunzira Baibulo akuganiza?
3 Tizidziwa Zimene Munthuyo Akuganiza: Kuti tidziwe ngati wophunzira Baibulo akumvetsa zimene akuphunzira komanso kuzikhulupirira, tiyenera kupewa kumangolankhula tokha. M’malomwake, tizimulimbikitsa kuti azinena maganizo ake. (Yak. 1:19) Tingadzifunse kuti, ‘Kodi munthuyu wamvetsa zimene Baibulo likunena pa nkhaniyi? Kodi angakwanitse kufotokoza bwinobwino nkhaniyi m’mawu akeake? Kodi akuona kuti zimene waphunzirazi n’zoona? Kodi amaona kuti zimene Baibulo limaphunzitsa n’zotheka kuzitsatira? (1 Ates. 2:13) Kodi akuona kufunika kogwiritsa ntchito zimene waphunzirazi pa moyo wake?’ (Akol. 3:10) Kuti tipeze mayankho a mafunso amenewa, tingafunike kuti tizifunsa mafunso othandiza wophunzirayo kunena maganizo ake, ndipo akamayankha, tizimvetsera.—Mat. 16:13-16.
4. Kodi tingatani ngati wophunzira Baibulo sakumvetsa zimene akuphunzira komanso sakuzitsatira pa moyo wake?
4 Nthawi zina pamatenga nthawi kuti munthu asiye makhalidwe oipa komanso kuti asiye kukhulupirira ziphunzitso zabodza zimene wakhala akuzikhulupirira. (2 Akor. 10:5) Koma kodi tingatani ngati wophunzirayo sakuvomereza kuti zimene akuphunzirazo n’zoona? Nanga tingatani ngati sakugwiritsa ntchito zimene akuphunzirazo pa moyo wake? Tiyenera kukhala oleza mtima. Tizikumbukira kuti pamatenga nthawi kuti Mawu a Mulungu komanso mzimu woyera uyambe kugwira ntchito pa munthu. (1 Akor. 3:6, 7; Aheb. 4:12) Ngati wophunzirayo sakumvetsa mutu winawake ndipo sakugwiritsa ntchito mfundozo pa moyo wake, ndi bwino kupita pa mutu wina m’malo momukakamiza kuti asinthe. M’kupita kwa nthawi, angayambe kusintha moyo wake ngati ataona kuti timamulezera mtima komanso kumukonda.