Ndandanda ya Mlungu wa May 24
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 24
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv mutu 7 ndime 10-19 ndi bokosi patsamba 81
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Samueli 13-15
Na. 1: 2 Samueli 13:23-33
Na. 2: Kodi Tiyenera Kugwiritsa Ntchito Zifaniziro Polambira Mulungu Woona? (rs tsa. 435 ndime 4 mpaka ndime 8)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Sitiyenera Kugwiritsa Ntchito Dzikoli Mokwanira, Kapena Kuti Mopitirira Malire? (1 Akor. 7:31)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Konzekerani Kudzagawira magazini mu June. Nkhani yokambirana ndi omvetsera. Fotokozani zimene zili m’magaziniwo kwa mphindi imodzi kapena ziwiri. Kenako sankhani nkhani zina, ndipo pemphani omvetsera kuti anene mafunso ndiponso malemba amene angagwiritsire ntchito pogawira magaziniwo. Chitani chitsanzo chosonyeza zimene tingachite pogawira magazini iliyonse.
Mph. 20: “Upainiya Ungakuyenereni Kwabasi!” Nkhani ya mafunso ndi mayankho.