Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/05 tsamba 3
  • Ino Ndiyo Nthawi Yofunika Kulalikira!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ino Ndiyo Nthawi Yofunika Kulalikira!
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Apainiya Amapereka ndi Kulandira Madalitso
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Madalitso a Utumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1997
  • “Upainiya Ungakuyenereni Kwabasi!”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Kodi Mungalowe pa “Khomo la Ntchito Yaikulu”?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 8/05 tsamba 3

Ino Ndiyo Nthawi Yofunika Kulalikira!

1. N’chifukwa chiyani inoyi ili nthawi yofunika kulalikira?

1 “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero.” Motsogozedwa ndi angelo, uthenga umenewu ukulengezedwa “kwa mtundu uliwonse, ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” Chifukwa chiyani? ‘Pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake [Mulungu].’ Lerolino, tikukhala mu “nthawi ya chiweruziro,” imene idzatifikitsa ku chiwonongeko cha dongosolo lino la zinthu. N’kofunika kwambiri kuti anthu ‘alambire Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.’ Palibe ntchito iliyonse imene ingakhale yofunika ndiponso yofuna changu kwambiri kuposa ntchito yolalikira “Uthenga Wabwino wosatha.” Inde, ino ndiyo nthawi yofunika kulalikira!—Chiv. 14:6, 7.

2. Pozindikira za nthawi imene tikukhalayi, kodi atumiki a Yehova amasonyeza motani kuti ali atcheru?

2 Zaka khumi zapitazo, atumiki a Yehova anagwira ntchito pafupifupi maola 12 biliyoni mu ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. Ambiri asintha moyo wawo kuti akhale ndi nthawi yambiri ya kututa kwauzimu kumeneku. (Mat. 9:37, 38) Mwachitsanzo, chaka chatha, ofalitsa oposa 850,000 anatumikira monga apainiya mwezi uliwonse. Kwa apainiya okhazikika, izi zikutanthauza kuti amayembekezeka kupereka maola 70 mwezi uliwonse. Pamene apainiya othandiza amafunikira kugwira ntchito kwa maola 50 mu utumiki wa kumunda.

3. Kodi ndi kusintha kotani kumene ofalitsa nthawi zambiri amafunikira kupanga kuti akwanitse kuchita upainiya?

3 Zofunika Kuti Munthu Achite Upainiya: Podziwa kuti “yafupika nthawi,” apainiya akuyesetsa kukhala ndi moyo wosafuna zambiri. (1 Akor 7:29, 31) Amayesetsa kupeza njira zosawononga ndalama zambiri n’cholinga chakuti asamagwire ntchito yolembedwa kwa nthawi yaitali. Mwachitsanzo, ena asamukira m’nyumba zocheperapo. Enanso achotsa zinthu zosafunika kwenikweni zimene anali nazo. (Mat. 6:19-21) Nthawi zambiri, amafunikiranso kuchepetsa zolinga za m’moyo wawo. Amachita zonsezi ndi cholinga chakuti akhale ndi nthawi yochitira utumiki ndi mtima wonse. (Aef. 5:15, 16) Pokhala anthu akhama, odzimana, ndiponso odalira Yehova, ofalitsa ambiri apanga ndandanda yabwino imene yawathandiza kuchita upainiya.

4. Kodi n’zinthu zothandiza ziti zimene mungachite kuti mukwanitse kuchita upainiya?

4 Kodi mungathe kuchita upainiya? Bwanji osapempha apainiya amene amachita bwino kuti akuuzeni mmene amachitira? Yendani nawo mu utumiki wa kumunda kuti muone chimwemwe chimene iwo amapeza. Werengani nkhani zokhudza upainiya zimene zatuluka mu zofalitsa zathu. Khalani ndi zolinga zotheka zimene zingadzakuthandizeni kuchita upainiya. Ngati pali zinthu zinazake zimene zikukulepheretsani kuchita upainiya, muuzeni Yehova m’pemphero, ndipo m’pempheni kuti akuthandizeni kulimbana nazo.—Miy. 16:3.

5. Kodi kuchita upainiya kumatithandiza motani kusula luso lathu mu utumiki?

5 Madalitso ndi Chimwemwe Zimene Timapeza: Upainiya umatithandiza kusula luso lathu logwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, ndipo zimenezi zimadzetsa chimwemwe. “Limakhala dalitso lalikulu kwambiri ngati munthu amatha kulunjika nawo bwino mawu a choonadi,” anafotokoza choncho mpainiya wina wachitsikana. “Ukamachita upainiya, umagwiritsa ntchito Baibulo kwambiri. Panopa ndikamapita khomo ndi khomo, ndimatha kukumbukira malemba oyenerera kwa mwininyumba aliyense.”—2 Tim. 2:15.

6. Kodi kuchita upainiya kumatiphunzitsa chiyani?

6 Kuchita upainiya kumatiphunzitsanso luso losiyanasiyana lofunika pa moyo. Kumathandiza achinyamata kudziwa kugwiritsa ntchito nthawi mwanzeru, kugwiritsa ntchito bwino ndalama, ndiponso kugwirizana ndi anthu ena. Ambiri amayamba kuona zinthu pa moyo ndi maso auzimu chifukwa cha upainiya. (Aef. 4:13) Ndiponso, apainiya ali ndi mwayi woona dzanja la Yehova likuwachitira zambiri pa moyo wawo.—Mac. 11:21; Afil. 4:11-13.

7. Kodi upainiya umatithandiza motani kuyandikana ndi Yehova?

7 N’kutheka kuti limodzi la madalitso aakulu kwambiri a kuchita upainiya n’lakuti umatithandiza kuyandikana ndi Yehova. Izi zingatithandize kuti tipirire ziyeso. Mlongo wina amene anapirira mavuto aakulu kwa nthawi yaitali anati: “Ubwenzi wanga ndi Yehova, umene ndaukulitsa mwa kuchita upainiya, unandithandiza kupirira mavuto anga onse.” Anatinso: “Ndili wokondwa kuti moyo wanga wonse monga munthu wachikulire, ndatumikira Yehova mu utumiki wa nthawi zonse. Izi zandithandiza kuti ndidzipereke kutumikira mwa njira zimene sindinaganizire poyamba.” (Mac. 20:35) Nafenso tingapeze madalitso titadzipereka pa ntchito yofunika imeneyi yolalikira ufumu.—Miy. 10:22.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena