Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/07 tsamba 4
  • Kodi Mungalowe pa “Khomo la Ntchito Yaikulu”?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungalowe pa “Khomo la Ntchito Yaikulu”?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nthawi Ina Munakhalapo Mpainiya Wokhazikika?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Ino Ndiyo Nthawi Yofunika Kulalikira!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • “Upainiya Ungakuyenereni Kwabasi!”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Apainiya Amapereka ndi Kulandira Madalitso
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 6/07 tsamba 4

Kodi Mungalowe pa “Khomo la Ntchito Yaikulu”?

1. Kodi ndi “khomo la ntchito yaikulu” lotani limene latitsegukira?

1 “Khomo la ntchito yaikulu” litam’tsegukira mtumwi Paulo, iyeyo anaona kuti ndi mwayi wopitiriza kuchita ntchito yolalikira mofunitsitsa ngakhale kuti anthu ambiri ankamutsutsa. (1 Akor. 16:9) Masiku ano, ofalitsa Ufumu okwana 642,000 padziko lonse alowa pa khomo la ntchito yaikulu mwa kukhala apainiya okhazikika.

2. N’chifukwa chiyani ndi bwino kuunika moyo wathu nthawi ndi nthawi?

2 Zinthu Zimasintha: Ngakhale kuti sitingachite zambiri panopa chifukwa cha mmene moyo wathu ulili, zinthu zingasinthe. Motero, ndi bwino kuti nthawi ndi nthawi tiziunika moyo wathu ndipo tisamangodikira mpaka zinthu zitakhala bwinobwino. (Mlal. 11:4) Kodi ndinu wachinyamata yemwe wangotsala pang’ono kumaliza maphunziro a kusekondale? Kodi ndinu kholo limene lili ndi ana omwe adzayamba sukulu posachedwa? Kodi mwangotsala ndi nthawi yochepa kuti mupume pa ntchito? Kusintha kwa moyo kotereku kungakupatseni nthawi yowonjezereka yoti muyambe utumiki waupainiya wokhazikika. Mlongo wina amene kale ankadwaladwala anasankha kukhala mpainiya ali ndi zaka 89. N’chifukwa chiyani anatero? Chifukwa panali patadutsa chaka chimodzi osagonekedwa ku chipatala ndipo anaona kuti thanzi lake linali bwinopo.

3. Kodi anthu ena asintha zinthu motani pamoyo wawo kuti akhale apainiya okhazikika?

3 Poyamba, Paulo anali ndi cholinga choti akaone abale ake ku Korinto. Koma anasintha maganizo ake chifukwa cha uthenga wabwino wa Ufumu. Masiku anonso, anthu ambiri amene ndi apainiya okhazikika anasintha zinthu zambiri pamoyo wawo n’cholinga chochita upainiya. Apainiya ena asintha zinthu kuti akhale ndi moyo wosafuna zambiri moti amangogwira ntchito ya maola ochepa kuti apeze zofunika pamoyo. Ndipo iwowo amasangalala kwambiri ndi mwayi wawo wotumikira. (1 Tim. 6:6-8) Mabanja ena asintha zinthu kuti mwamuna yekha azigwira ntchito ndipo zimenezi zathandiza kuti mkazi ayambe upainiya.

4. Kodi tingatani ngati tikuona kuti sitingakwanitse maola ofunikira?

4 Musafulumire kuganiza kuti simungachite upainiya chifukwa simungakwanitse maola ofunikira. Mumangofunikira maola pafupifupi awiri ndi theka patsiku. Ngati mukuona kuti simungakwanitse, yesani kuchita upainiya wothandiza mwezi umodzi kapena iwiri muli ndi cholinga chokwaniritsa maola 70. Zimenezi zingakuthandizeni kulawa ubwino wa upainiya. (Sal. 34:8) Lankhulani ndi omwe akuchita upainiya panopa. N’kutheka kuti iwowa anathetsa mavuto ofanana ndi amene mukukumana nawo. (Miy. 15:22) Pemphani Yehova kuti adalitse kuyesayesa kwanu kuchita zambiri muutumiki.—1 Yoh. 5:14.

5. N’chifukwa chiyani upainiya ndi ntchito yopindulitsa?

5 Ntchito Yopindulitsa: Kukhala mpainiya wokhazikika kumabweretsa madalitso ambiri. Mumatha kukhala wosangalala chifukwa choti nthawi zonse mumapatsa ena mwa kuwalalikira. (Mac. 20:35) Upainiya ungakuthandizeni kukhala ndi luso lolondoloza bwino kwambiri Mawu a Mulungu. (2 Tim. 2:15) Ndipo mumatha kukhala ndi mwayi wambiri woona kuti dzanja la Yehova likukuthandizani. (Mac. 11:21; Afil. 4:11-13) Upainiya umakuthandizaninso kukhala ndi makhalidwe auzimu monga kupirira, ndipo mumatha kuyandikira kwambiri kwa Yehova. (Yak. 4:8) Kodi inuyo mungalowe pa khomo la ntchito yaikulu ndi kukhala mpainiya wokhazikika?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena