Kodi Nthawi Ina Munakhalapo Mpainiya Wokhazikika?
1. Kodi abale ndi alongo ambiri akhala ndi mwayi wotani, nanga ena anayenera kuchita chiyani?
1 Kwa zaka zambiri, abale ndi alongo ambiri akhala akuchita utumiki wa nthawi zonse ‘wophunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino.’ (Mac. 5:42) Komabe, ena anasiya kuchita upainiya pa zifukwa zosiyanasiyana. Ngati munachitapo upainiya wokhazikika, kodi mwaonanso mmene zinthu zilili pa moyo wanu kuti muone ngati mungayambirenso kuchita utumikiwu?
2. N’chifukwa chiyani anthu amene anachitapo upainiya ayenera kuganiziranso mmene panopo zinthu zilili pa moyo wawo?
2 Zinthu Zimasintha: Kodi zimene zinakuchititsani kusiyana upainiya zilipobe? Mwachitsanzo, ngati munasiya upainiya chifukwa chakuti simunkakwanitsa maola 90 pa mwezi, kodi panopa mukhoza kuyambiranso pamene maola ofunika pa mwezi anachepetsedwa kufika pa 70? Kodi simukukhalanso wopanikizika ku ntchito kapena udindo wosamalira banja wachepa kuchokera pa nthawi imene munasiya upainiya? Mlongo wina amene anasiyana upainiya chifukwa chodwaladwala anayambiranso upainiya ali ndi zaka 89. Iye anali asanagonekedwenso m’chipatala kwa chaka chimodzi ndipo anaona kuti akhoza kuyambiranso kuchita upainiya.
3. Kodi banja lingachite chiyani kuti wina m’banjalo achite upainiya?
3 Mwina simunachitepo upainiya, koma winawake m’banja lanu anasiya kuchita upainiya kuti azitha kusamalira winawake m’banjalo, monga kholo lokalamba. (1 Tim. 5:4, 8) Ngati zili choncho, kodi pali zimene inuyo kapena ena m’banjalo mungachite kuti muthandize amene anasiya upainiyayo? Bwanji osakambirana nkhani imeneyi? (Miy. 15:22) Anthu m’banja akachita zinthu mogwirizana kuti wina achite upainiya, onse amamva kuti athandizapo.
4. Kodi mungachite chiyani ngati panopo simungathe kuyambiranso kuchita upainiya?
4 Musagwe ulesi ngati zinthu sizikuyenda bwino pa moyo wanu kuti muyambirenso kuchita upainiya. Mtima wofuna kuchita upainiya umasangalatsa Yehova. (2 Akor. 8:12) Muzigwiritsa ntchito luso limene munapeza pamene munkachita upainiya. Muziuza Mulungu zolinga zanu m’pemphero, komanso muziyesetsa kugwiritsa ntchito mipata imene mumapeza kuti musinthe zinthu pa moyo wanu. (1 Yoh. 5:14) Mwina m’tsogolomu, Yehova adzakutsegulirani “khomo lalikulu la mwayi wautumiki kuti mudzachitenso upainiya wokhazikika womwe ndi wosangalatsa.”—1 Akor. 16:9.