Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
Okondedwa Anzathu a Mboni za Yehova:
Tikukhala mu nthawi yofunika kwambiri, ndipotu ndife osangalala kwabasi. Tikusangalalanso kwambiri kugwira nanu ntchito limodzi inu abale ndi alongo okondedwa pamene ‘tikutumikira mogwirizana’ Atate wathu wakumwamba Yehova, pogwira ntchito yochitira umboni za iye imene sinachitikepo ndi kale lonse.—Zef. 3:9; Yoh. 14:12.
Ngakhale kuti timasangalala potumikira Yehova, sizikutanthauza kuti tilibe mavuto. M’chaka chautumiki chapitachi, ena mwa inu mwakumana ndi mavuto chifukwa cha zivomezi, kusefukira kwa madzi, mphepo zamkuntho, ndi masoka ena achilengedwe oopsa kwambiri. (Mat. 24:7) Ambiri akuvutika ndi matenda aakulu ndiponso ukalamba. Tonsefe tikuvutika chifukwa cha kuwonjezeka kwa ‘zowawa ngati za pobereka.” (Mat. 24:8) M’mayiko angapo, kuphatikizapo dziko la Armenia, Eritrea, ndi South Korea, abale anthu ambiri anatsekeredwa m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo.—Mat. 24:9.
Kodi chatithandiza n’chiyani kuti tikhalebe ndi maganizo abwino ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto amenewa? Lemba lachaka cha 2010 latikumbutsa mfundo yofunika kwambiri yakuti: ‘Chikondi chimapirira zinthu zonse. Chikondi sichitha.’ (1 Akor. 13:7, 8) Inde, chikondi chathu pa Yehova ndiponso kukondana kwathu kumatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira.
Anthu ambiri amene amati ndi Akhristu amadabwa kwambiri ndi khama lathu pa ntchito yolalikira. Ngakhale kuti nthawi zina angatsutse zimene timakhulupirira ndiponso zimene timaphunzitsa, ena akakamizika kunena kuti, “Anthu inu mukugwira ntchito imene ifeyo tiyenera kugwira.” Kodi n’chiyani chimene chimalimbikitsa Mboni za Yehova kupitiriza kulalikira tsiku ndi tsiku? Yankho la funso limeneli ndi chikondi. Mofanana ndi Atate wathu wakumwamba, sitifuna kuti wina aliyense adzawonongedwe. (2 Pet. 3:9) Cholinga chathu chofuna kuti anthu onse alape chikuonekera tikaona chiwerengero cha ofalitsa cha chaka chautumiki chapitachi. Ofalitsa onse anakwana 7,508,050. Chimenechi ndi chiwerengero chapamwamba kuposa ziwerengero zonse za m’mbuyomu. Kodi ndi gulu linanso liti lachipembedzo limene lili ndi anthu ambiri chonchi amene amadzipereka ndi mtima wonse chifukwa cha chikondi chawo, kugwira ntchito yolalikira kuti athandize ena mwauzimu?
Timalimbikitsidwa kuona kuti ulosi wa Yesaya ukupitiriza kukwaniritsidwa. Iye analemba kuti: “M’masiku otsiriza, phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa nsonga za mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa mapiri ang’onoang’ono. Mitundu yonse idzakhamukira kumeneko.” (Yes. 2:2-4) Pakati pa anthu amene akukhamukira ku nyumba ya Yehova pali anthu 294,368 amene anabatizidwa m’chaka chautumiki chapitachi. Ndife osangalala kulandira anthu amtengo wapatali amenewa m’gulu lathu. Chikondi chathu chachikhristu chitilimbikitsetu kupitiriza kuthandiza anthu amenewa kulimbana ndi mdani wathu Satana Mdyerekezi.—1 Pet. 5:8, 9.
Chiwerengero chapamwamba kuposa ziwerengero za m’mbuyomu cha anthu okwana 18,706,895 amene anapezeka pa Chikumbutso Lachiwiri pa March 30, 2010, chikusonyeza kuti pali anthu mamiliyoni ambiri amene akhoza kugwirizana nafe pa kulambira Yehova. Ndife osangalala kuti Yehova sanaweruzebe dongosolo lazinthu loipali. Padakali pano, chikondi chikutithandiza kuti tipitirize kupirira.—2 Ates. 3:5.
Misonkhano Yachigawo ya mutu wakuti, “Khalanibe pa Ubwenzi ndi Yehova” imene yambiri inachitika m’chaka cha 2010 padziko lonse, inalimbitsa ubwenzi wathu ndi Atate wathu wakumwamba Yehova. Zimenezitu n’zogwirizana kwambiri ndi mawu a wamasalimo akuti: “Odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.” (Sal. 144:15) Kaya m’tsogolomu muchitika zotani, tili ndi chikhulupiriro kuti ngati Yehova ali nafe, palibe chimene tingaope. (Sal. 23:4) Posachedwapa, Yehova, kudzera mwa mwana wake, ‘awononga ntchito za Mdyerekezi.’ (1 Yoh. 3:8) Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imeneyo. Koma padakali pano, tili ndi ntchito yambiri yoti tichite imene ikutipangitsa kukhala otanganidwa.—1 Akor. 15:58.
Dziwani kuti “nthawi zonse” timakutchulani m’mapemphero athu. (Aroma 1:9) Choncho, “pitirizani kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kukukondani. Chitani zimenezi pamene mukuyembekezera kuti chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chidzakutsegulireni njira yoti mulandirire moyo wosatha.”—Yuda 21.
Dziwani kuti timakukondani nonsenu.
Ndife abale anu,
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova.