Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/11 tsamba 5-6
  • Uzilemekeza Yehova ndi Zinthu Zako Zamtengo Wapatali—Gawo 3

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Uzilemekeza Yehova ndi Zinthu Zako Zamtengo Wapatali—Gawo 3
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
km 3/11 tsamba 5-6

Uzilemekeza Yehova ndi Zinthu Zako Zamtengo Wapatali—Gawo 3

1. Tchulani dzina la bokosi lachitatu.

1 Bokosi lachitatu limene tikambirane ndi lolembedwa kuti, “Zopereka za Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu Padziko Lonse.” Kodi tingagwiritse ntchito bwanji bokosi limeneli?

2. N’chifukwa chiyani pakufunikira Nyumba za Ufumu zambiri chaka chilichonse m’Malawi muno?

2 Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu Padziko Lonse: Ngakhale kuti Nyumba za Ufumu zamangidwa zambiri m’Malawi muno zaka zingapo zapitazi, pakadali mipingo imene ilibe Nyumba za Ufumu. Chaka chilichonse, mipingo yatsopano ikupangidwa. Ina mwa mipingo imeneyi imasonkhana m’Nyumba ya Ufumu imodzi ndi mpingo wina. Komabe, kumene zimenezi n’zosatheka, Nyumba za Ufumu zatsopano ziyenera kumangidwa. Chifukwa cha kupangidwa kwa mipingoku, pakufunika kumanga Nyumba za Ufumu zokwana 30 m’Malawi muno chaka chilichonse.

3. Kodi tizigwiritsa ntchito bwanji bokosi lotchedwa “Zopereka za Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu Padziko Lonse”?

3 Pofuna kuthandiza mipingo imene ilibe Nyumba ya Ufumu yawoyawo, tingapereke zopereka m’bokosi lolembedwa kuti “Zopereka za Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu Padziko Lonse.” Ndalama zimenezi zikafika ku ofesi ya nthambi, amazigwiritsa ntchito pothandiza mipingo mwa njira imeneyi.

4. (a) Kodi nkhani ya mbali zitatuyi yatithandiza bwanji? (b) Fotokozani mwachidule mmene timagwiritsira ntchito bokosi lililonse la zopereka.

4 Nkhani yokhala ndi zigawo zitatuyi yatithandiza kuona kuti bokosi lililonse la zopereka lili ndi cholinga chake ndipo mabokosiwa si ofanana. Taona kuti bokosi lotchedwa kuti “Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse-Mateyu 24:14” limathandiza pa ntchito yolalikira padziko lonse. Timagwiritsanso ntchito bokosi limeneli tikafuna kupereka ndalama poyamikira mabuku ndi zofalitsa zina. Ndalama zimene zimaperekedwa m’bokosi la “Zopereka Zothandiza Pampingo” zimagwira ntchito za pampingo. Ndalamazi zimagwira ntchito monga kulipirira magetsi, madzi, kukonzetsa zinthu zowonongeka pa Nyumba ya Ufumu, kulipira inshuwalansi ya Nyumba ya Ufumu, kuchirikiza woyang’anira dera pamene akuchezera mpingo, komanso kuthandizira thumba la dera pakafunika kutero. Tikamafuna kuyamikira mwayi umene tili nawo wokhala ndi Nyumba ya Ufumu yathuyathu, timapereka ndalama m’bokosi limeneli, mogwirizana ndi zimene tinalonjeza, kenako kumapeto kwa mwezi uliwonse, ndalamazi zimatumizidwa ku ofesi ya nthambi. Ndiyeno tili ndi bokosi lolembedwa kuti, “Zopereka za Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu pa Dziko Lonse” limene talifotokoza m’ndime 2 ndi 3 m’nkhani ino.

5. Kodi lemba la Miyambo 11:25 likutitsimikizira chiyani?

5 Choncho, aliyense wa ife ayenera kuganizira zimene angachite kuti tichirikize kulambira koona mwa kuponya zopereka m’mabokosi a zoperekawa. Mosakayikira, tikachita zonse zimene tingathe, malinga ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu, Yehova adzatidalitsa. Werengani Miyambo 11:25. Tiyenitu tonsefe tilemekeze Yehova ndi zinthu zathu zamtengo wapatali.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena