Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/11 tsamba 6-7
  • Kutumikira Yehova Kumatilemeretsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutumikira Yehova Kumatilemeretsa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
km 3/11 tsamba 6-7

Kutumikira Yehova Kumatilemeretsa

1 Lemba la Miyambo 10:22 limati: “Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa, ndipo sawonjezerapo ululu.” Kunena zoona, timasangalala tikamaona kuti moyo wauzimu wa atumiki a Yehova amasiku ano ukuyenda bwino. Tiyeni tikambirane mbali zina zimene zikuyenda bwino mwauzimu ndiponso phindu lake kwa ifeyo patokha.

2 Kudziwa Zolondola Zimene Baibulo Limaphunzitsa: Matchalitchi Achikhristu amanena kuti amakhulupirira Baibulo. Koma sagwirizana pa zimene limaphunzitsa. Ngakhale anthu a chipembedzo chimodzi nthawi zambiri amasiyana maganizo pa zimene kwenikweni Malemba amaphunzitsa. Komatu zimenezi n’zosiyana ndi atumiki a Yehova. Ngakhale kuti ndife osiyana mayiko, zikhalidwe, kapena mafuko, timalambira Mulungu amene timamudziwa ndi dzina lake. Mulungu ameneyu si milungu itatu mwa mulungu mmodzi. (Deut. 6:4; Sal. 83:18; Maliko 12:29) Timadziwanso kuti nkhani yaikulu yakuti Mulungu ndiye woyenera kulamulira yatsala pang’ono kuthetsedwa ndiponso kuti tikapitiriza kukhala okhulupirika kwa Mulungu, aliyense wa ife amakhudzidwa ndi nkhani imeneyi. Tikudziwa zoona za anthu amene anafa ndipo sitiopa Mulungu amene anthu ena amati amazunza anthu ku moto kapena ku puligatoliyo.—Mlal. 9:5, 10.

3 Timamasuka ku zizolowezi ndi makhalidwe oipa: Nkhani zofotokoza kuopsa kwa kusuta, kumwa mowa mwauchidakwa ndiponso khalidwe lachiwerewere n’zofala kwambiri m’manyuzipepala ndiponso pa wailesi. Komatu nthawi zambiri anthu salabadira mauthenga amenewa. Nanga chimachitika n’chiyani munthu wa mtima wabwino akaphunzira kuti Mulungu woona amadana ndi zinthu zimenezi ndiponso kuti amakhumudwa ndi anthu amene amachita makhalidwe amenewa? Iye amasiya kuchita makhalidwewa. (Yes. 63:10; 1 Akor. 6:9, 10; 2 Akor. 7:1; Aef. 4:30) Ngakhale kuti kwenikweni amachita zimenezi kuti akondweretse Yehova Mulungu, amapezanso madalitso ena omwe ndi thanzi labwinopo ndiponso mtendere wa m’maganizo.

4 Moyo wabanja wosangalala: M’mayiko ambiri mabanja sakuyenda bwino. Mabanja ambiri akutha, zimene zikuchititsa kuti nthawi zambiri ana azikhala okhumudwa ndiponso amantha. M’mayiko ena ku Ulaya, mabanja 20 pa mabanja 100 aliwonse ndi a kholo limodzi. Kodi Yehova watithandiza bwanji kukhala okhulupirika pa nkhani imeneyi? Tiyeni tiwerengere limodzi Aefeso 5:22–6:4. Pamene tikuwerenga lembali tione malangizo abwino amene Mawu a Mulungu akuuza amuna okwatira, akazi okwatiwa ndi ana. Kutsatira zimene zafotokozedwa pa lembali ndiponso m’Malemba ena kumalimbitsa mabanja, kumathandiza makolo kulera bwinobwino ana awo, komanso kumachititsa moyo wabanja kukhala wosangalatsa. Kodi sitikusangalala ndi madalitso amenewa?

5 Maphunziro ofunika ndiponso othandiza kwambiri: Gerhard ndi mkulu mu mpingo wa Mboni za Yehova. Pofotokoza zimene zinamuchitikira ali mwana, iye anati: “Ndili mwana, ndinkavutika kwambiri kulankhula. Ndikapanikizika, ndinkalephera kulankhula ndipo ndinkachita chibwibwi. Ndinkadziona kuti ndine munthu wachabechabe. Makolo anga anakonza zoti ndipite kusukulu yophunzitsa kulankhula, koma zimenezi sizinathandize ngakhale pang’ono. Vuto langa linali la m’maganizo. Ndinapeza thandizo kuchokera kwa Yehova kudzera m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Kulembetsa m’sukulu imeneyi kunandilimbikitsa kwambiri. Ndinachita khama kwambiri kutsatira zimene ndinkaphunzira ndipo zimenezi zinandithandiza. Ndinakhala womasuka, ndinasiya kudandaula, ndiponso ndinayamba kulimba mtima mu utumiki. Tsopano ndimakamba nkhani za onse. Ndikuthokoza Yehova, amene wandithandiza kudzera m’sukulu imeneyi.” Kunena zoona, timasangalala kwambiri ndi mmene Yehova amatiphunzitsira kuti tichite ntchito yake.

6 Kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ndiponso ubale wa padziko lonse: Katrin, amene amakhala ku Germany, anada nkhawa kwambiri atamva za chivomezi chimene chinachititsa tsunami kumwera chakum’mawa kwa Asia. Pa nthawi imene tsokali linachitika n’kuti mwana wake wamkazi atapita kukacheza kudziko la Thailand. Kwa maola 32, mayi ameneyu sanadziwe kuti mwana wake ali moyo kapena ali pa gulu la anthu amene anafa kapena kuvulala omwe chiwerengero chawo chinkawonjezeka ola lililonse. Pamapeto pake mtima wa Katrin unakhala pansi atalandira telefoni yomutsimikizira kuti mwana wake ali bwino.

7 Kodi chinathandiza Katrin nthawi yovutayi n’chiyani? Iye anati: “Pafupifupi nthawi yonseyi ndinkangokhalira kupemphera kwa Yehova. Zimenezi zinkandichititsa kupeza mphamvu ndiponso kukhala ndi mtendere wa m’maganizo. Komanso abale achikondi auzimu anabwera kudzandiona ndipo anandilimbikitsa.” (Afil. 4:6, 7) Zikanakhalatu zovuta kwambiri kwa mayiyu akanakhala kuti sanalimbikitsidwe ndi pemphero kwa Yehova komanso abale achikondi auzimu. Kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi Mwana wake limodzi ndi abale anthu achikhristu ndi dalitso lapadera ndiponso lamtengo wapatali moti sitiyenera kulipeputsa ngakhale pang’ono.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena